Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 116

Kukoma Mtima Ndi Kofunika Kwambiri

Kukoma Mtima Ndi Kofunika Kwambiri

(Aefeso 4:​32)

  1. 1. Tikukutamandani Yehova,

    Mwatipatsa Mawu.

    Taona nzeru zanu zakuya

    Ndi kukoma mtima kwanu.

  2. 2. Yesu akuuza ovutika

    Apite kwa iye.

    Akanyamule goli lakelo

    Kuti atsitsimulidwe.

  3. 3. Mulungu wathu ndi Mwana wake

    Ndi okoma mtima.

    Nafe tikhale okoma mtima.

    Tizilimbikitsa ena.