Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 130

Muzikhululuka

Muzikhululuka

(Salimo 86:5)

  1. 1. Mwachikondi M’lungu

    Anapereka Yesu

    Kuti tikhululukidwe

    Ndi kudzathetsa imfa.

    M’lungu amakhululuka

    Ngati ife talapa.

    Nsembe ya dipo ya Yesu

    Imatithandizadi.

  2. 2. Tikamatsanzira

    Chifundo cha Yehova

    Pokhululukira anthu,

    Tidzakhululukidwa.

    Tikhale ololerana

    Ndipo tisamadane.

    Tizilemekeza onse

    Komanso kuwakonda.

  3. 3. Chifundo n’chabwino,

    Tonse tikhale nacho.

    Sitidzasunga zifukwa

    Tikakhumudwitsidwa.

    Tikatsanzira Yehova

    Yemwe ndi wachikondi,

    Tidzakhululukirana.

    Tidzafanana naye.