Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 142

Tigwire Mwamphamvu Chiyembekezo Chathu

Tigwire Mwamphamvu Chiyembekezo Chathu

(Aheberi 6:​18, 19)

  1. 1. Anthu akhala akuyenda mumdima

    Ndipo sizikuwathandiza n’komwe.

    Zadziwika kuti anthu ochimwa

    Sangathetse kuvutikaku.

    (KOLASI)

    Tiziimba mwachisangalalo

    Poti Ufumu wa M’lungu wayamba.

    Yesu adzachotsadi zoipa.

    Tigwire mwamphamvu chiyembekezo.

  2. 2. Uthenga womwe ukumveka ndi woti

    ‘Tsiku la Mulungu layandikira.’

    Anthu sadzakhalanso ndi chisoni.

    Tiyeni tiimbire M’lungu.

    (KOLASI)

    Tiziimba mwachisangalalo

    Poti Ufumu wa M’lungu wayamba.

    Yesu adzachotsadi zoipa.

    Tigwire mwamphamvu chiyembekezo.