Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 146

“Zinthu Zonse Zimene Ndikupanga Ndi Zatsopano”

“Zinthu Zonse Zimene Ndikupanga Ndi Zatsopano”

(Chivumbulutso 21:​1-5)

  1. 1. Zizindikiro zikusonyezadi

    Kuti Yesu akulamulira.

    Anachotsa Satana kumwamba,

    Posachedwa am’chotsa padziko.

    (KOLASI)

    Sangalalani chifukwa

    Mulungu alidi nafe.

    Iye adzachotsatu imfayi,

    Chisoni ndiponso zopweteka.

    Zonse zidzakhala zatsopano.

    Mawuwa ndi oona.

  2. 2. Ona Yerusalemu watsopano.

    Mkwatibwi wa Mwanawankhosayo

    Atavala mochititsa chidwi.

    Yehova ndiye kuwala kwake.

    (KOLASI)

    Sangalalani chifukwa

    Mulungu alidi nafe.

    Iye adzachotsatu imfayi,

    Chisoni ndiponso zopweteka.

    Zonse zidzakhala zatsopano.

    Mawuwa ndi oona.

  3. 3. Mzindawu udzasangalatsa anthu.

    Uzidzakhala wosatsekedwa.

    Anthu azidzayenda mowala.

    Atumikinu muziwalabe.

    (KOLASI)

    Sangalalani chifukwa

    Mulungu alidi nafe.

    Iye adzachotsatu imfayi,

    Chisoni ndiponso zopweteka.

    Zonse zidzakhala zatsopano.

    Mawuwa ndi oona.