NYIMBO 148
Yehova Amapereka Populumukira
-
1. Yehova ndinudi Mulungu wamoyo.
Mphamvu zaoneka
M’chilengedwe chonse.
Palibe M’lungu wina
angachite zimene
Inu mumachita.
(KOLASI)
Yehova ndiye pothawira pathu.
Timaonadi kuti iye ndi Thanthwe.
Tilengeze molimba mtima
mphamvu zake.
Tithawire kwa Yehovayo,
tim’tamande.
-
2. Zingwe za imfa zikandizungulira
Ndidalira inu.
Mundipatse mphamvu,
Mundilimbitse mtima,
mumve kulira kwanga.
M’lungu ndibiseni.
(KOLASI)
Yehova ndiye pothawira pathu.
Timaonadi kuti iye ndi Thanthwe.
Tilengeze molimba mtima
mphamvu zake.
Tithawire kwa Yehovayo,
tim’tamande.
-
3. Mudzamveka ngati mabingu
kumwamba.
Adani anuwo
Adzanjenjemera.
Mudzakhala chimene
mukufuna kukhala.
Onse adzaona.
(KOLASI)
Yehova ndiye pothawira pathu.
Timaonadi kuti iye ndi Thanthwe.
Tilengeze molimba mtima
mphamvu zake.
Tithawire kwa Yehovayo,
tim’tamande.
(Onaninso Sal. 18:1, 2; 144:1, 2.)