Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 158

“Sadzachedwa”

“Sadzachedwa”

(Habakuku 2:3)

  1. 1. Dziko lopanda

    nkhawa zonsezi

    Ndi lomwe tonse

    tikulakalaka.

    Padziko lonse

    zinthu zaipa

    Tikudziwatu

    muthetsa zonsezi.

    (KOLASI)

    Molezadi mtima

    tikudikirira

    Dzikotu latsopano.

    Mapeto afika

    posachedwa pompa.

    Mawu anu akuti,

    ‘sadzachedwadi.’

  2. 2. Mulungu wathu

    mudzaitana

    Omwe anafa, ndipo

    adzadzuka.

    Zidzakhalatu

    zosangalatsa!

    Tithandizeni

    kulezabe mtima.

    (KOLASI)

    Molezadi mtima

    tikudikirira

    Dzikotu latsopano.

    Mapeto afika

    posachedwa pompa.

    Mawu anu akuti,

    ‘sadzachedwadi.’

  3. 3. Mumafufuza

    mitima yathu

    N’kutitonthoza ndi

    chiyembekezo.

    Tichite khama

    polalikira.

    Tikhale maso

    nthawi yafupika.

    (KOLASI)

    Molezadi mtima

    tikudikirira

    Dzikotu latsopano.

    Mapeto afika

    posachedwa pompa.

    Mawu anu akuti,

    ‘sadzachedwadi.’

    Tiyembekezerebe.

(Onaninso Akol. 1:11.)