Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 4

“Yehova Ndi M’busa Wanga”

“Yehova Ndi M’busa Wanga”

(Salimo 23)

  1. 1. Yehova ndi M’busa wanga

    Sindidzasowa kanthu.

    Amadziwa zofuna zanga

    Zomwe ndi zofunika.

    Amanditsogolelanso

    M’malo otetezeka.

    Mwachikondi chakedi chosatha

    Wandipatsa mtendere.

    Mwachikondi chake chosatha

    Wandipatsa mtendere.

  2. 2. Zochita zanu n’zabwino,

    Zonse n’zachilungamo.

    Zochita zanga nthawi zonse

    Zikulemekezeni.

    Pamene ndikuvutika

    Mumandithandizadi.

    Sindidzaopatu chilichonse

    Chifukwa muli nane.

    Sindidzaopa chilichonse

    Chifukwa muli nane.

  3. 3. M’lungu ndinu M’busa wanga,

    Ndidzakutsatirani.

    Mumandilimbikitsa ndithu.

    Mumandipatsa zonse.

    Poti ndinudi wamphamvu

    Ndimakudalirani.

    Kukoma mtima kwanu kosatha

    Muzindisonyezabe.

    Kukoma mtimatu kosatha

    Muzindisonyezabe.

(Onaninso Sal. 28:9; 80:1.)