Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 48

Tiziyenda ndi Yehova Tsiku Lililonse

Tiziyenda ndi Yehova Tsiku Lililonse

(Mika 6:8)

  1. 1. Timayenda ndi Yehova

    Nthawi zonse modzichepetsa.

    Amatikomera mtima

    Tikamamusangalatsadi.

    Mwa nsembe ya Yesu Khristu,

    Tingayende ndi M’lungu.

    Choncho timadzipereka

    Potumikira Yehova.

  2. 2. Mapeto ali pafupi

    Ndipo Satana ndi wokwiya.

    Timatsutsidwa kwambiri

    Choncho tingamachite mantha.

    Yehova atiteteza

    Ngati timamumvera.

    Tizimutumikirabe

    Ndi kum’konda nthawi zonse.

  3. 3. M’lungu amatithandiza

    Ndi mzimu ndi mawu akenso.

    Iye amatithandiza

    Kudzeranso mu mpingo wake.

    Tikayenda ndi Yehova

    Tidzachita zabwino.

    Choncho tikhulupirike

    N’kukhala odzichepetsa.