NYIMBO 64
Tizigwira Ntchito Yokolola Mosangalala
-
1 .Tili munthawi yokolola,
Ndi nthawidi yapadera.
M’mundamo tirigu wachamo
Tiyeni tikakolole.
Yesu akutitsogolera,
Ndi chitsanzodi chabwino.
Ndi mwayi wapadera kwambiri
Kugwira nawo ntchitoyi.
-
2. Timakonda M’lungu ndi anthu
Choncho timachita khama.
Tiphunzitse anthu mwachangu,
Mapeto ayandikira.
Yehova amatidalitsa,
Timakhala ndi chimwemwe.
Tipirire pogwira ntchitoyi
M’lungu adzatithandiza.
(Onaninso Mat. 24:13; 1 Akor. 3:9; 2 Tim. 4:2.)