Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 66

Lengezani Uthenga Wabwino

Lengezani Uthenga Wabwino

(Chivumbulutso 14:​6, 7)

  1. 1. Poyamba sitinkadziwa za Ufumu.

    Pano tadziwa

    Mfumu yolonjezedwa.

    Mwa chifundo ndi chikondi cha Yehova

    Anaganizira anthu ochimwafe.

    Anakonza zoti pakhale Ufumu

    Ndipo wolamulira waketu ndi Yesu.

    Anakonzanso za kagulu ka nkhosa

    Kodzakhala mkwatibwi wa Mwana wake.

  2. 2. Uthenga wabwinowu tisaubise,

    M’lungu akufuna anthu audziwe.

    Angelo amatithandiza kwambiri

    Pogwira ntchito

    yolengeza Ufumu.

    Tapatsidwa udindo ndiponso mwayi

    Wom’tamanda ndi kuyeretsa dzina lake.

    Tikwaniritse udindo umenewu

    Mwa kulalikira uthenga wabwino.