Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 73

Tithandizeni Kukhala Olimba Mtima

Tithandizeni Kukhala Olimba Mtima

(Machitidwe 4:​29)

  1. 1. Polalikira Ufumu

    Komanso dzina lanu,

    Anthu ena amatsutsa

    Ndiponso kutinyoza.

    Koma sitiwaopa

    Timamvera inu nokha.

    Choncho Yehova tikupempha

    Mutipatse mzimu wanu.

    (KOLASI)

    Polalikira uthenga

    Mutichotsere mantha.

    Tikhale olimba mtima,

    Anthu amve uthenga.

    Amagedo ikufika,

    Tikhale olimba mtima.

    Tithandizeni Yehova,

    Tikupempha.

  2. 2. Pomwe tikuchita mantha

    M’madziwa ndife fumbi.

    Mudzatithandiza ndithu

    Paja munalonjeza.

    Imvani kuopseza

    Kwa anthu odana nafe.

    Tithandizeni tisaope.

    Tikhale olimba mtima.

    (KOLASI)

    Polalikira uthenga

    Mutichotsere mantha.

    Tikhale olimba mtima,

    Anthu amve uthenga.

    Amagedo ikufika,

    Tikhale olimba mtima.

    Tithandizeni Yehova,

    Tikupempha.