Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 92

Malo Odziwika Ndi Dzina Lanu

Malo Odziwika Ndi Dzina Lanu

(1 Mbiri 29:16)

  1. 1. Yehova tinali ndi mwayi

    Okumangirani nyumba.

    Tikukupatsani tsopano.

    Dzina lanu lidziwike.

    Zonse zomwe timapereka

    Zimakhala zanu zomwe.

    Luso, mphamvu ndi chuma chathu,

    Tazipereka kwa inu.

    (KOLASI)

    Tikupereka malowa

    Kuti mudziwikedi.

    Tikupereka malowa,

    Chonde alandireni.

  2. 2. Tikulemekeza inuyo

    Pokutamandani pano.

    Landirani ulemerero

    Tikamachuluka muno.

    Malowa tikukupatsani

    Ndipo tiziwasamala,

    Kuti apereke umboni

    Za dzina lanu loyera.

    (KOLASI)

    Tikupereka malowa

    Kuti mudziwikedi.

    Tikupereka malowa,

    Chonde alandireni.