NYIMBO 99
Abale Ambirimbiri
-
1. Abale ambirimbiri.
Inde ochuluka.
Aliyense ndi mboni
Yokhulupirika.
Tilipodi ambiri.
Tikuchulukabe.
Tachokera m’mayiko onse
Ndi mitundu yonse.
-
2. Abale ambirimbiri.
Timalalikira
Uthenga wabwinowu
Kwa ofuna kumva.
Pamene tafooka
Yesu atipatsa
Mpumulo ndi mphamvu zambiri.
Sitimada nkhawa.
-
3. Abale ambirimbiri.
Timatetezedwa
Potumikira M’lungu
Padziko lapansi.
Tilipodi ambiri.
Timalalikira.
Timagwira ntchito ndi M’lungu
Pomutumikira.
(Onaninso Yes. 52:7; Mat. 11:29; Chiv. 7:15.)