Kukhala Mwamtendere M’dziko Lopanda Mtendere
Pangani Dawunilodi:
1. Paliponse ndimaona kuti anthu ndi okwiyatu.
Ndi olemedwa ndi nkhawa za tsiku lililonse.
Mawu a Mulungu amati ndikhale wodekha.
Ndikapemphera chamumtima ndimakhala ndi mtendere.
(KOLASI)
Kukhala mwamtendere n’kovuta, koma tikayesetsa
Tidzasangalaladi m’Paradaiso, ndi mtendere wochuluka.
2. Olo kuntchito sikulephera kukhala mikangano.
Ndiyesetse kudzigwira n’kukhalabe wodekha.
Ndikumbukire kuti panopa moyo ukuvuta.
Ena ndi okwiya chifukwa akukumana ndi zokhoma.
(KOLASI)
Kukhala mwamtendere n’kovuta, koma tikayesetsa
Tidzasangalaladi m’Paradaiso, ndi mtendere wochuluka.
(VESI LOKOMETSERA)
Ndizovuta kukhala
M’dziko lopanda mtendere.
Koma Mulungu wa mtendere
Amateteza mitima.
3. Nthawi yolalikira yakwana tili khomo ndi khomo.
Anamva zabodza zokhudza Mboni ndiye akubangula.
Talalikira momveka bwino tingathe kutsanzika.
Alibetu chidwi chenicheni tichoke mwamtendere.