Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“M’patseni Yehova Ulemerero”

“M’patseni Yehova Ulemerero”

(Salimo 96:8)

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Yehova, palibe munthu

    Angafanane nanu.

    N’dzakubwezerani chani

    Pa zonse mumandipatsa?

    Ndikayang’ana kumwamba,

    Ndimaonatu mphamvu.

    Ndine wotsika Yehova

    Koma m’mandiganizira.

    (KOLASI)

    Ndikuimba, ndimveni Yehova.

    Ndikukutamandani.

    M’lungu wanga, Mfumu yamuyaya.

    Ndinu woyeneradi

    Ulemerero wonse.

  2. 2. Zochita zanga Yehova

    Zikulemekezeni.

    Ndizilengeza uthenga

    Ndi ntchito zanu zabwino.

    Kukutumikiranitu

    Kumandisangalatsa.

    Muzindipatsabe mphamvu

    Muzinditsogolerabe.

    (KOLASI)

    Ndikuimba, ndimveni Yehova.

    Ndikukutamandani.

    M’lungu wanga, Mfumu yamuyaya.

    Ndinu woyeneradi

    Ulemerero wonse.

  3. 3. Nyanja, zitunda ndi zigwa,

    Dzuwa, mwezi, nyenyezi,

    Zimanditsimikizira

    Chikondi chanu chosatha.

    Ulemu ndi kukongola

    Ndi zomwe ndimaona.

    Sindingachitire mwina

    Koma kukulambirani.

    (KOLASI)

    Ndikuimba, ndimveni Yehova.

    Ndikukutamandani.

    M’lungu wanga, Mfumu yamuyaya.

    Ndinu woyeneradi

    Ulemerero wonse.