Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizikhutira

Tizikhutira

Pangani Dawunilodi

  1. 1. Tikaona zokongola,

    Tingafune titakhala nazo. 

    Koma titati tizigule

    Tingadzakhale kapolo.

    (KOLASI)

    Tizikhutira

    Adzatisamalira.

    Tizikhutira, tim’dalire.

    Tizikhutira

    Tisakhale kapolo.

    Tizikhutira, tim’dalire.

  2. 2. Tilitu ndi pogona,

    Chakudya ndi zovala.

    Tikamakhutira ndi zochepa 

    Tizikhala ndi mtendere.

    (KOLASI)

    Tizikhutira 

    Adzatisamalira.

    Tizikhutira, tim’dalire.

    Tizikhutira

    Tisakhale kapolo.

    Tizikhutira, tim’dalire. 

    (VESI LOKOMETSERA)

    Amatisamalira,

    Sangatikhumudwitse.

    Ndipo amatikonda,

    Tisamatekeseke.

    Tingamudalire.

  3. 3. Moyo wosalira zambiriwu

    Timasangalala ndi mtendere.

    Sitilemedwa n’kusaka chuma,

    Timatumikira M’lungu.

    (KOLASI)

    Tizikhutira

    Adzatisamalira.

    Tizikhutira, tim’dalire.

    Tizikhutira

    Tisakhale kapolo.

    Tizikhutira.

    (KOLASI)

    Tizikhutira

    Adzatisamalira.

    Tizikhutira, tim’dalire.

    Tizikhutira

    Tisakhale kapolo.

    Tizikhutira, tim’dalire.