Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chilengedwe Chanu Chimandidabwitsa

Chilengedwe Chanu Chimandidabwitsa

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Ndikumvatu mbalame zikuimba.

    Nyenyezi zikubisika m’mene kukucha.

    Dzuwa nalo likukongolanso,

    Kamphepo kabwinodi, m’nyengo yotentha.

    (KUKONZEKERA KOLASI)

    Ndimuimbire, Yehova M’lungu,

    Ntchito zakezi n’zazikulu.

    N’zodadwitsatu kuti amatisamalira.

    (KOLASI)

    Poona izi, ndithu ndiimba.

    Poona izi, ndithu ndiimba.

    Ndiimbadi.

  2. 2. Zamoyo zonse ndi zodabwitsa​—

    Usiku ndi masana zimalankhulatu

    M’mapiri mpakatu pansi pa Nyanja

    Zamoyo zonsezi zim’tamandedi.

    (KUKONZEKERA KOLASI)

    Ndimuimbire, Yehova M’lungu,

    Ntchito zakezi n’zazikulu.

    N’zodadwitsatu kuti amatisamalira.

    (KOLASI)

    Poona izi, ndithu ndiimba.

    Poona izi, ndithu ndiimba.

    Ndiimbadi.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Zomwe timatha kuzionazi

    Zimatithandizatu kum’dziwa mlengi wathu.

    (KUKONZEKERA KOLASI)

    Ndimuimbire, Yehova M’lungu,

    Ntchito zakezi n’zazikulu.

    N’zodadwitsatu kuti amatisamalira.

    (KOLASI)

    Poona izi, ndithu ndiimba.

    Poona izi, ndithu ndiimba.

    Poona izi, ndithu ndiimba.

    Poona izi, ndithu—di ndiimba.

    Poona izi, ndithu—di ndiimba.

    Ndiimbadi.