Dziko Latsopano Lili Pafupi
Pangani Dawunilodi:
1.Mbalametu zikuimba,
Mitambo ikuyenda.
Mukudutsa pachidikha
Ndipo dzuwa likuwalanso.
Akufa akuuka,
Ngati mukungolota.
Dziko la Paradaiso
Linalidi pafupi.
2.Muchidikha muli nyumba
Ina ili pa phiri.
Anthu akuimba nyimbo
Mumtsinje madzi akuyenda.
Mbewu zachanso m’minda.
Ndi nthawi yokolora.
Dziko lokongolali
Linalidi pafupi.
(VESI LOKOMETSERA)
Tiziuza anzathunso
Zomwe tikuyembekeza.
Sikudzakhala kulira.
Zinthu zonse n’zatsopano.
3.Anthu akusangalala
Kafungo ka zomera.
Mukuitanitsa ‘nzanu
Pamene tsiku likuyamba.
Tikuthokoza Yehova,
Posonyeza chikondi.
Madalitso onsewa
Analidi pafupi.
(VESI LOKOMETSERA)
Ndikaona nkhope yanu,
Ikumandimwetulira.
Sindinkaganiza n’komwe
Kuti tidzakumananso.
4.Dziko latsopano
Ndikuliyembekeza.
Ndi lonjezo la Yehova.
Ndipo lidzakwaniritsidwa.
Ndikaganizira izi
Sindimadanso nkhawa.
Chifukwatu dzikolo,
Lilitu pafupi zedi.