Muziphunzira Kuti Mukhale Olimba
Pangani Dawunilodi:
1. Kungoyambiratu tili makanda.
Tinkaphunzira komanso kumazimvetsa.
N’sanagone bambo ankawerenga.
Pano ndakula ndimawerengabe ndekha.
Ndipo ndikafatsa ndimatengatu bukulo.
Ndimakumbukira zomwe n’nawerenga kuti n’khale wolimba.
(KOLASI)
Muziphunzira,
Udzalimba ngati mtengo wa m’madzi.
Muziphunzira.
Zinthu zonsetu zidzakuyendera.
Muziphunzira.
Monga mtengo wa mizu yakuya.
Muziphunzira.
Udzakula n’kumaona zinthu zonse.
2. Ndingatani anzanga akandifunsa.
Za zinthu zomwe ndimazikhulupirira.
Zimenezitu sizingandivute.
Kuyambira ndili mwana ndinkaphunzira.
Ndipo ndikafatsa ndimatengatu bukulo.
Ndimakumbukira zomwe n’nawerenga kuti n’khale wolimba.
(KOLASI)
Muziphunzira,
Udzalimba ngati mtengo wa m’madzi.
Muziphunzira.
Zinthu zonsetu zidzakuyendera.
Muziphunzira.
Monga mtengo wa mizu yakuya.
Muziphunzira.
Udzakula n’kumaona zinthu zonse.
(VESI LOKOMETSERA)
Zomwe ndimawerenga
Ndizigwiritsa ntchito
Kuthandiza ena komanso kuwalimbikitsa.
(KOLASI)
Muziphunzira.
Muziphunzira.
Muziphunzira.
Muziphunzira.
Muziphunzira.
Udzalimba ngati mtengo wa m’madzi.
Muziphunzira.
Zinthu zonsetu zidzakuyendera
Muziphunzira,
Monga mtengo wa mizu yakuya.
Muziphunzira.
Udzakula n’kumaona zinthu zonse.