Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndikusintha

Ndikusintha

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Zomwe ndikuona​—

    Nthawi zonse

    Utumiki wanga

    Pano n’chizolowezi.

    Zafika pochita mwamwambo chabe.

    Ndikuyeneratu kusintha​—

    M’peze njira zina.

    (KOLASI)

    Ndikusintha momwe ndimachitira.

    Ndiyese njira zatsopano.

    Yehova, ndadziwa zoyenera.

    Lero ndikusintha, n’kudalireni.

  2. 2. M’pofunika khama,

    Ndaonatu

    Mmene kusinthaku

    Kwandithandiziradi.

    Nditayesera njirazi ndalimba.

    Makomo anatsegukanso,

    Koma sin’nadziweko.

    (KOLASI)

    Ndikusintha momwe ndimachitira.

    Ndiyese njira zatsopano.

    Yehova, ndadziwa zoyenera.

    Lero ndikusintha, n’kudalireni.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Ndinkaganiza kuti

    Sizingan’chitikire.

    Pena sindimvetsadi,

    Zinachitika.

    Ndapeza madalitso

    Nditalimbadi mtima.

    Ndipo mtsogolo muno

    N’dzadalitsidwabe.

    (KOLASI)

    Ndikuyesera njira zatsopano.

    N’nazolowerazi ndisinthe.

    Yehova, ndadziwa zoyenera.

    Nditakudalirani, mwandidalitsa.

    (KOLASI)

    Ndikusintha momwe ndimachitira.

    Ndiyese njira zatsopano.

    Yehova, ndadziwa zoyenera.

    Lero ndikusintha.

    (KOLASI)

    Ndikusintha momwe ndimachitira.

    Ndiyese njira zatsopano.

    Yehova, ndadziwa zoyenera.

    Lero ndikusintha, n’kudalireni​—

    N’kudalireni.