Sindidzasiya
Pangani Dawunilodi:
1. Atate nthawitu yakwana
Ndichite zomwe Yesu ananena:
‘Ngati ndinazunzidwa, mudzazunzidwanso.’
Sizodabwitsa, sizachilendonso.
Yehova ndapempha n’thandizeni.
Moyo wanga ndapereka kwa inu.
Musaiwale zomwe ndachita.
Ndidzakhulupirika nthawi zonse.
Ponyozedwa ndi pozunzidwanso
Chifukwatu cha dzina lanulo
Ndimaona kuti uwu ndi mwayi,
Ndatsimikizadi ndisafooke.
(KOLASI)
Kutumikira Yehova
Sindisiya ndipo sin’ngasinthe.
Limbitseni, n’thandizeni,
Ndikhulupirire inu.
Sin’dzasiya.
2. Mwandidalira, n’kudalirani.
Mayeserowa ndaolokadi.
Mafumu, achibale ndi anzanga
Ndatsimikiza ’sandilepheretse.
(KOLASI)
Kutumikira Yehova
Sindisiya ndipo sin’ngasinthe.
Limbitseni, n’thandizeni,
Ndikhulupirire inu.
Kutumikira Yehova
Sindisiya ndipo sin’ngasinthe.
Limbitseni, n’thandizeni,
Ndikhulupirire inu.
Sin’dzasiya.