Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tiziyamikira Chilengedwe cha Mulungu

Tiziyamikira Chilengedwe cha Mulungu

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Maluwa ’kukula m’mwamba mwa phiri,

    Mapiri akukongola chapatali,

    Kadzuwanso kakuwala bwino,

    Mbalame zikuuluka.

    (KUKONZEKERA KOLASI)

    N’napangidwa

    Modabwitsa

    Kodi nditani

    Kuti ndim’thokoze?

    (KOLASI)

    Ndizimuthokoza,

    Ndimuuze M’lungu

    Zikomotu

    Amatikondadi.

    N’kayang’ana,

    N’kuziganizira ntchito za Yehova.

    Ndim’thokoze pa chilichonse.

    Ndiziyamikira.

    Ndiziyamikira.

  2. 2. Kumwamba kukuchita kukongola,

    Mitundu yokongola mochititsa chidwi.

    Kaphokoso ka mtsinje kotsitsimula,

    Nyenyezi ndi mwezi zikuwala.

    (KUKONZEKERA KOLASI)

    N’napangidwa

    Modabwitsa

    Ndadziwa zochita

    Kuti ndim’thokoze.

    (KOLASI)

    Ndizimuthokoza,

    Ndimuuze M’lungu

    Zikomotu

    Amatikondadi.

    N’kayang’ana,

    N’kuziganizira ntchito za Yehova,

    Ndim’thokoze pa chilichonse.

    Ndiziyamikira.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Ndaona nzeru ndi mphamvu,

    Ubwino wanu m’zonse,

    N’chikondi chanu.

    Ndikuthokoza;

    Ndiziyamikira.

    (KOLASI)

    Ndizimuthokoza,

    Ndimuuze M’lungu

    Zikomotu

    Amatikondadi.

    N’kayang’ana,

    N’kuziganizira ntchito za Yehova,

    Ndim’thokoze pa chilichonse.

    Ndiziyamikira.

    Ndiziyamikira.

    Tiziyamikira.