Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsiku Lililonse Lili N’zodetsa Nkhawa Zake

Tsiku Lililonse Lili N’zodetsa Nkhawa Zake

Pangani Dawunilodi:

  1. 1.Za dziko latsopano ndikudziwa ndithu,

    Ndikukhulupiriradi mavuto adzatha.

    Koma pena ndi zovuta,

    Kuona malonjezowo,

    Ndi chikondi cha Mulungu ndikakhala m’mavuto.

    Koma Yehova ’lipo.

    (KOLASI)

    Ndimapemphera kwa M’lungu.

    Ndikakhalatu ndi nkhawa,

    N’dalire mphamvu zake.

    Yehovatu ali nane.

    Wandipatsa mawuwa.

    Ndi anzanga abwino.

    Tsiku lililonse lili n’zake.

    Ndiye ndisadzitopetse,

    Ndisaganizire zamawa.

    Zamawa n’zina

    Ndisade nkhawa.

  2. 2. Mvera malangizo anga,

    Ndimakukonda.

    Ganizira zabwino,

    Osati mavutowa.

    Zomwe M’lungu wachita.

    Anaperekatu Yesu.

    Um’khulupirire ndithu.

    Watipatsatu zambiri.

    Ndiye usaope.

    (KOLASI)

    Tim’pemphe Yehova.

    Tikakhalatu ndi nkhawa,

    Timudalire ndithu.

    Yehovatu ali nafe.

    Watipatsa mawuwa

    Ndi anzathu abwino.

    Tsiku lililonse lili n’zake

    Ndiye tisadzitopetse.

    Tisaganizire zamawa;

    Zamawa n’zina;

    Tisade nkhawa.

    (KOLASI)

    Tim’pemphe Yehova.

    Tikakhalatu ndi nkhawa,

    Timudalire ndithu.

    Yehova ali nafe.

    Watipatsa mawuwa

    Ndi anzathu abwino.

    Tsiku lililonse lili n’zake.

    Ndiye usadzitopetse;

    Usaganizire zamawa.

    Zamawa n’zina

    Usade nkhawa​—

    Tisade nkhawa.