Wokondedwa Wanga
Pangani Dawunilodi:
1. Mphatso ina yochoka m’mwamba,
Ndikupeza womukonda.
Kupeza munthu woyenera,
Nthawi yapadera yafika.
(KOLASI)
Ndikudziwa ndithu kuti n’zotheka.
N’zingwe zitatu,
M’banjamo.
Yehova atitsogolere pa zonse,
N’zosangalatsadi kupeza
Wokondedwawe,
Wokondedwawe.
2. Tingavutike,
Chikondichi chizikulabe.
Tidzagwirizana mpaka kale.
Tidzakondanabe moyo wonse.
O! Moyo wonse.
(KOLASI)
Tikudziwa ndithu kuti n’zotheka.
N’zingwe zitatu,
M’banjamo.
Yehova atitsogolere pa zonse,
N’zosangalatsadi kupeza
Wokondedwawe,
Wokondedwawe.
(VESI LOKOMETSERA)
Palibe chiononge,
Mphatso yochokera kwa Mulunguyi.
‘Chikondi n’champhamvudi ngati imfa.’
‘Ndiwe fupa langa, ndiwe mnofu wanga’
Mkazi wabwino zedi, m’zochita zako.
Ndidzakukonda moyo wonse.
3. Ndikufunatu udziwe
Chikondi changa n’chenicheni.
N’nasangalala kukukwatira.
Ndikuthokoza pondikonda.
Indedi.
(KOLASI)
Tikudziwa ndithu kuti n’zotheka.
N’zingwe zitatu,
M’banjamo.
Yehova atitsogolere pa zonse,
N’zosangalatsadi kupeza
Wokondedwawe,
Wokondedwawe.
N’zosangalatsadi kupeza
Wokondedwawe.