Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

TIMABUKU TOTHANDIZA ANTHU KUTIDZIWA BWINO PADZIKO LONSE

A Mboni za Yehova Komanso Mmene Amaonera Chithandizo Chachipatala

A Mboni za Yehova Komanso Mmene Amaonera Chithandizo Chachipatala

A Mboni za Yehova amaona kuti moyo ndi mphatso yamtengo wapatali imene Mulungu anawapatsa. Amaona kuti moyo komanso magazi ndi zinthu zopatulika. Choncho akadwala amapita kuchipatala kuti akalandire thandizo la mankhwala ndipo amachita zinthu mogwirizana ndi madokotala komanso anthu ena amene akuwathandiza n’cholinga choti apatsidwe thandizo labwino kwambiri popanda kuikidwa magazi.