Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

TIMABUKU TOTHANDIZA ANTHU KUTIDZIWA BWINO PADZIKO LONSE

A Mboni za Yehova Komanso Ntchito Yawo Yolalikira

A Mboni za Yehova Komanso Ntchito Yawo Yolalikira

A Mboni za Yehova amaona kuti kuuza ena zimene amakhulupirira ndi mbali yofunika kwambiri ya kulambira kwawo. Iwo amachita zimenezi polalikira uthenga wabwino wa m’Baibulo kwa anthu omwe amakhala nawo pafupi. Kodi amagwiritsa ntchito njira ziti, nanga ntchito yawoyi imathandiza bwanji anthu m’madera omwe amakhala?