Kuona Malo ku Beteli
Tikukuitanani kuti mudzaone maofesi athu a nthambi omwenso amadziwika kuti Beteli. Ku maofesi athu ena kulinso malo achionetsero omwe mukhoza kuona nokha popanda wokutsogolerani.
Kuyambiranso Kuona Malo: M'mayiko ambiri, anthu adzayambiranso kuona malo m'maofesi athu a nthambi kuyambira pa 1 June, 2023. Kuti mudziwe zambiri, lankhulani ndi abale a ku nthambi yomwe mukufuna kukaonayo. Komabe, musapite kukaona malo ngati mwapezeka ndi COVID-19 kapena ngati muli ndi zizindikiro za chimfine kapenanso ngati posachedwapa munakumana ndi munthu amene wapezeka ndi COVID-19.
Côte d’Ivoire
Rue J-58 - Lot 1758
Deux-Plateaux
3ème tranche, Vallon
ABIDJAN
CÔTE D’IVOIRE
+225 2241-3606
Kuona Malo
Lolemba mpaka Lachisanu
2:00 p.m. mpaka 4:00 p.m.
Nthawi yonse: Ola limodzi
Zimene Timachita
Timamasulira mabuku ofotokoza Baibulo m’Chibaule komanso m’zinenero zina 6. Zinenerozi ndi Chiataye, Chibete, Chigouro, Chiguere ndi Chiyakuba. Timajambulanso masewero ndiponso mabuku ochita kuwerengedwa, omwe anthu angamvetsere m’zinenero zambiri.