Pitani ku nkhani yake

Kuona Malo ku Beteli

Tikukuitanani kuti mudzaone maofesi athu a nthambi omwenso amadziwika kuti Beteli. Ku maofesi athu ena kulinso malo achionetsero omwe mukhoza kuona nokha popanda wokutsogolerani.

Kuyambiranso Kuona Malo: M'mayiko ambiri, anthu adzayambiranso kuona malo m'maofesi athu a nthambi kuyambira pa 1 June, 2023. Kuti mudziwe zambiri, lankhulani ndi abale a ku nthambi yomwe mukufuna kukaonayo. Komabe, musapite kukaona malo ngati mwapezeka ndi COVID-19 kapena ngati muli ndi zizindikiro za chimfine kapenanso ngati posachedwapa munakumana ndi munthu amene wapezeka ndi COVID-19.

Italy

Congregazione Cristiana Dei Testimoni di Geova

Via della Bufalotta 1281

I-00138 ROME RM

ITALY

+39 06-872941

Kuona Malo

Lolemba mpaka Lachisanu

8:00 a.m. mpaka 10:30 a.m. ndi 1:00 p.m. mpaka 3:30 p.m.

Nthawi yonse: Ola limodzi

Zimene Timachita

Timamasulira mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo m’Chitaliyana ndi Chinenero Chamanja cha ku Italy. Timajambulanso zinthu zina zomvetsera komanso mavidiyo. Timayang’anira ntchito imene timagulu ndiponso mipingo yoposa 3,000 ya Mboni za Yehova ikugwira ku Italy ndi kumayiko ena.

Koperani pepala losonyeza ofesi yathu.