Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kuona Malo ku Beteli

Tikukuitanani kuti mudzaone maofesi athu a nthambi omwenso amadziwika kuti Beteli. Ku maofesi athu ena kulinso malo achionetsero omwe mukhoza kuona nokha popanda wokutsogolerani.

Kuyambiranso Kuona Malo: M'mayiko ambiri, anthu adzayambiranso kuona malo m'maofesi athu a nthambi kuyambira pa 1 June, 2023. Kuti mudziwe zambiri, lankhulani ndi abale a ku nthambi yomwe mukufuna kukaonayo. Komabe, musapite kukaona malo ngati mwapezeka ndi COVID-19 kapena ngati muli ndi zizindikiro za chimfine kapenanso ngati posachedwapa munakumana ndi munthu amene wapezeka ndi COVID-19.

Kenya

Elgeyo Marakwet Rd

Kilimani area near Adams Arcade

NAIROBI

KENYA

+254 20-387-3211

+254 20-387-3212

+254 20-387-3213

Kuona Malo

Lolemba mpaka Lachisanu

8:00 a.m. mpaka 11:00 a.m. ndi 1:00 p.m. mpaka 4:00 p.m.

Nthawi yonse: Ola limodzi ndi hafu

Zimene Timachita

Timayang’anira ntchito yomasulira mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo m’zinenero 10, kuphatikizapo Chinenero Chamanja cha ku Kenya. Timajambulanso mavidiyo ndi zinthu zina zomvetsera m’zinenero za ku Kenya. Timathandizira pa ntchito imene Mboni za Yehova zikugwira m’mayiko ena oyandikana ndi dziko la Kenya.

Koperani pepala losonyeza ofesi yathu.