Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kuona Malo ku Beteli

Tikukuitanani kuti mudzaone maofesi athu a nthambi omwenso amadziwika kuti Beteli. Ku maofesi athu ena kulinso malo achionetsero omwe mukhoza kuona nokha popanda wokutsogolerani.

Kuyambiranso Kuona Malo: M'mayiko ambiri, anthu adzayambiranso kuona malo m'maofesi athu a nthambi kuyambira pa 1 June, 2023. Kuti mudziwe zambiri, lankhulani ndi abale a ku nthambi yomwe mukufuna kukaonayo. Komabe, musapite kukaona malo ngati mwapezeka ndi COVID-19 kapena ngati muli ndi zizindikiro za chimfine kapenanso ngati posachedwapa munakumana ndi munthu amene wapezeka ndi COVID-19.

Venezuela

Av. Intercomunal La Victoria-El Consejo

Frente a La Mora II

LA VICTORIA 2121 ESTADO ARAGUA

VENEZUELA

+58 244-400-5000

Kuona Malo

Lolemba mpaka Lachisanu

8:00 a.m. mpaka 11:00 a.m. ndi 1:00 p.m. mpaka 4:00 p.m.

Nthawi yonse: Ola limodzi

Zimene Timachita

Timamasulira mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo m’Chinenero Chamanja cha ku Venezuela. Mwezi uliwonse, timatumiza kumipingo mabuku olemera matani 27 a m’zinenero 29. Timayang’anira ntchito imene Mboni za Yehova zoposa 125,000 zikugwira ku Venezuela.

Koperani pepala losonyeza ofesi yathu.