Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi a Mboni za Yehova Alipo Angati Padziko Lonse?

Kodi a Mboni za Yehova Alipo Angati Padziko Lonse?

Lipoti la Chaka a Chautumiki cha 2023

Chiwerengero cha Mboni za Yehova padziko lonse

8,816,562

Chiwerengero cha mipingo

118,177

A Mboni za Yehova amalalikira m’mayiko okwana

239

Kodi ndi anthu ati amene mumawawerenga kuti ndi a Mboni za Yehova?

Anthu okhawo amene amalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu mwezi uliwonse ndi amene timawawerenga kuti ndi a Mboni. (Mateyu 24:14) Amenewa akuphatikizapo anthu omwe anabatizidwa kuti akhale a Mboni ndiponso amene sanabatizidwe koma anavomerezedwa kuti azilalikira nawo.

Kodi munthu ayenera kupereka ndalama kuti akhale wa Mboni za Yehova?

Ayi. Munthu sayenera kupereka ndalama kuti awerengedwe kukhala wa Mboni kapena kuti apatsidwe udindo uliwonse m’gulu lathu. (Machitidwe 8:18-20) Nthawi zambiri munthu amene wapereka ndalama sadziwika. Wa Mboni aliyense amachita zonse zimene angathe pothandiza ntchito yolalikira. Amachita zimenezi pogwiritsa ntchito nthawi yake, mphamvu zake ndiponso popereka zinthu mwa kufuna kwake.​—2 Akorinto 9:7.

Kodi mumadziwa bwanji chiwerengero cha anthu amene amalalikira?

Mwezi uliwonse wa Mboni za Yehova aliyense amapereka lipoti kumpingo losonyeza zimene wachita polalikira. Munthu amapereka lipotili mwa kufuna kwake.

Malipoti onse a mpingo amaphatikizidwa palipoti limodzi ndipo amalitumiza ku ofesi ya nthambi ya m’dzikolo. Ndiyeno ofesi ya nthambi imaphatikiza pamodzi malipoti a mipingo yonse ya m’dzikolo ndipo amatumiza lipotili kulikulu lathu lapadziko lonse.

Chaka chautumiki b chikamatha, kulikulu lathu amagwiritsa ntchito malipotiwo kuti adziwe chiwerengero cha Mboni za Yehova m’dziko lililonse chaka chimenecho. Ndiyeno amaphatikiza ziwerengero zonsezi kuti adziwe chiwerengero cha Mboni za Yehova padziko lonse. Kenako amalemba mu Buku Lapachaka la Mboni za Yehova malipoti a dziko lililonse komanso zimene a Mboni anakumana nazo polalikira. Mofanana ndi Akhristu akale omwe anasangalala ndi malipoti a ntchito yawo, ifenso timalimbikitsidwa kwambiri tikawerenga malipotiwa.​—Machitidwe 2:41; 4:4; 15:3.

Kodi mumawerenganso anthu amene amasonkhana nanu koma salalikira?

Anthuwo sawerengedwa kuti ndi a Mboni za Yehova koma timawalandira akamabwera kudzasonkhana nafe. Ambiri a iwo amapezeka pamwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Khristu. Choncho tingadziwe chiwerengero chawo tikachotsa chiwerengero cha a Mboni pa chiwerengero cha opezeka pa Chikumbutso. Mu 2023, anthu okwana 20,461,767 anapezeka pa mwambowu.

Palinso anthu ambiri amene safika pamisonkhano yathu koma timaphunzira nawo Baibulo kwaulere. M’chaka cha 2023, tinachititsa maphunziro a Baibulo pafupifupi 7,281,212 mwezi uliwonse. Pa maphunziro ena, tinkaphunzitsa anthu angapo nthawi imodzi.

N’chifukwa chiyani boma limapeza chiwerengero chokwera cha a Mboni za Yehova kuposa chimene mumapeza?

A boma amapeza chiwerengero cha anthu omwe ali m’zipembedzo zosiyanasiyana, pofunsa anthuwo kuti atchule chipembedzo chawo. Mwachitsanzo, boma la ku United States linanena kuti pochita kalembera “limafufuza kuti lidziwe ngati anthu amaona kuti ali m’chipembedzo chinachake.” Bomali linanenanso kuti izi zimachititsa kuti lisapeze chiwerengero cholondola koma chiwerengero cha anthu omwe “amangoona kuti ali m’chipembedzocho.” Mosiyana ndi zimenezi, ife timawerenga kuti munthu ndi wa Mboni za Yehova akamalalikira komanso kupereka lipoti lake, osati munthu amene amangonena kuti ndi wa Mboni.

a Chaka chautumiki chimayambira pa September 1 ndipo chimatha pa August 31 m’chaka chotsatira. Mwachitsanzo, chaka chautumiki cha 2015 chinayamba pa September 1, 2014 ndipo chinatha pa August 31, 2015.

b Chaka chautumiki chimayambira pa September 1 ndipo chimatha pa August 31 m’chaka chotsatira. Mwachitsanzo, chaka chautumiki cha 2015 chinayamba pa September 1, 2014 ndipo chinatha pa August 31, 2015.