Kodi a Mboni za Yehova Amakakamiza Ana Awo Kuti Akhalenso a Mboni?
Ayi. Aliyense ali ndi ufulu wosankha pa nkhani yolambira Mulungu. (Aroma 14:12) A Mboni za Yehova amaphunzitsa ana awo mfundo za m’Baibulo, koma anawo akakula, aliyense amayenera kusankha yekha kuti akhale wa Mboni za Yehova kapena ayi.—Aroma 12:2; Agalatiya 6:5.
Mofanana ndi makolo ambiri, nawonso a Mboni za Yehova amafunira ana awo zabwino. Choncho amaphunzitsa anawo zinthu zomwe amaona kuti ndi zofunika monga, ntchito zosiyanasiyana, makhalidwe abwino komanso zimene amakhulupirira. Popeza kuti a Mboni za Yehova amakhulupirira kuti zimene Baibulo limaphunzitsa n’zimene zimathandiza anthu kukhala ndi moyo wosangalala, iwo amayesetsa kuphunzitsa ana awo Baibulo komanso kupita nawo kumisonkhano yawo. (Deuteronomo 6:6, 7) Komabe mwana aliyense akakula, amasankha yekha kutsatira zimene makolo ake amakhulupirira kapena ayi.
Kodi a Mboni za Yehova amabatiza ana akhanda?
Ayi. Baibulo silimanena kuti ana akhanda azibatizidwa. Mwachitsanzo, Baibulo limasonyeza kuti Akhristu a m’zaka 100 zoyambirira asanabatizidwe, choyamba anamvetsera uthenga, “analandira mawu” ndipo kenako analapa. (Machitidwe 2:14, 22, 38, 41) Choncho kuti munthu abatizidwe, ayenera kukhala wamkulu woti akhoza kumvetsa zomwe Baibulo limaphunzitsa, azikhulupirire komanso kuti asankhe kutsatira zomwe waphunzirazo. Mwana wakhanda sangathe kuchita zinthu zimenezi.
Ana akamakula, akhoza kusankha kuti abatizidwe. Komabe, kuti abatizidwe ayenera kumvetsa zomwe asankhazo.
Kodi a Mboni za Yehova amapewa kuchita zinthu ndi ana awo omwe asankha kuti asabatizidwe?
Ayi. Ngakhale kuti makolo a Mboni sangasangalale ngati mwana wawo sakukhulupirira zomwe iwo amakhulupirira, makolowo amapitirizabe kumukonda ndipo samasiya kuchita naye zinthu chifukwa choti sakufuna kukhala wa Mboni.
N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova amatenga ana awo pokalalikira?
A Mboni za Yehova amatenga ana awo akamapita kolalikira pa zifukwa zingapo. a
Baibulo limalimbikitsa makolo kuti aziphunzitsa ana awo zinthu zauzimu komanso kuwaphunzitsa kuti azilambira Mulungu. (Aefeso 6:4) Popeza kuti kulambira Mulungu kumaphatikizapo kuuza ena za chikhulupiriro chathu, ntchito yolalikira ndi njira imodzi yophunzitsira mwana.—Aroma 10:9, 10; Aheberi 13:15.
Baibulo limalimbikitsa ana kuti “atamande dzina la Yehova.” (Salimo 148:12, 13) Ndipo njira yabwino kwambiri yotamandira Mulungu ndi kuuza ena zokhudza Iye. b
Ana amaphunzira zambiri akamalalikira limodzi ndi makolo awo. Mwachitsanzo, amaphunzira kuyankhula ndi anthu osiyanasiyana, komanso amakhala ndi makhalidwe abwino monga chifundo, kukoma mtima, ulemu ndiponso kudzichepetsa. Amadziwanso bwino Malemba okhudza zomwe amakhulupirira.
Kodi a Mboni za Yehova amachita nawo maholide ndi zikondwerero zina?
A Mboni za Yehova sachita nawo maholide achipembedzo kapena zikondwerero zina zimene Mulungu sasangalala nazo. c (2 Akorinto 6:14-17; Aefeso 5:10) Mwachitsanzo, sitikondwerera masiku akubadwa komanso Khirisimasi chifukwa sizichokera m’Baibulo.
Komabe, timasangalala kucheza ndi mabanja athu komanso kupereka mphatso kwa ana athu. Nthawi iliyonse imene yapezeka, timacheza ndi achibale komanso kupatsana mphatso, osati pa masiku a holide okha.
a Ana amene makolo awo ndi a Mboni za Yehova, sapita kukalalikira popanda makolo awo kapena munthu wina wamkulu.
b Baibulo limafotokoza za ana ena omwe anasangalatsa Mulungu pofotokozera anthu ena zimene amakhulupirira.—2 Mafumu 5:1-3; Mateyu 21:15, 16; Luka 2:42, 46, 47.
c Onani nkhani yakuti “N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sachita Nawo Maholide Ena?”
d Mayina ena asinthidwa.