Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi Ndinu Akhristu?

Kodi Ndinu Akhristu?

 Inde. Ndife Akhristu pa zifukwa zotsatirazi:

  •   Timayesetsa kutsatira mosamala zimene Yesu Khristu ankaphunzitsa komanso khalidwe lake.—1 Petulo 2:21.

  •   Timakhulupirira kuti munthu angadzapulumuke pokhapokha ngati atakhulupirira Yesu chifukwa “palibe dzina lina pansi pa thambo, limene laperekedwa kwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.”—Machitidwe 4:12.

  •   Kuti munthu akhale wa Mboni za Yehova, amabatizidwa m’dzina la Yesu.—Mateyu 28:18, 19.

  •   Timapemphera m’dzina la Yesu.—Yohane 15:16.

  •   Timakhulupirira kuti Yesu ndi Mutu, kapena kuti munthu amene wapatsidwa udindo, pa munthu wina aliyense.—1 Akorinto 11:3.

 Komabe, ndife osiyana m’njira zambiri ndi zipembedzo zina zimene zimati n’zachikhristu. Mwachitsanzo, timakhulupirira kuti Baibulo limaphunzitsa zoti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, osati Mulungu mwana. (Maliko 12:29) Sitikhulupirira kuti munthu ali ndi mzimu umene umapitirizabe kukhala ndi moyo munthuyo akamwalira, komanso palibe pamene Malemba amasonyeza zoti Mulungu amazunza anthu powawotcha kumoto wosazima. Sitikhulupiriranso zakuti anthu amene amatsogolera mu mpingo ayenera kukhala ndi mayina audindo amene amawachititsa kukhala apamwamba mosiyana ndi anthu ena onse.—Mlaliki 9:5; Ezekieli 18:4; Mateyu 23:8-10.