Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi a Mboni za Yehova Amapereka Chakhumi?

Kodi a Mboni za Yehova Amapereka Chakhumi?

 Ayi, ife a Mboni za Yehova sitipereka chakhumi. Ndalama zimene zimathandizira kuti ntchito yathu iziyenda bwino ndi zimene anthu, omwe satchulidwa maina, amapereka mwa kufuna kwawo. Kodi chakhumi n’chiyani ndipo n’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova sapereka chakhumi?

 Lamulo loti anthu azipereka chakhumi, kapena kuti gawo limodzi mwa magawo 10 alionse a zinthu, linali m’gulu la Chilamulo chimene chinaperekedwa kumtundu wakale wa Isiraeli. Komabe, Baibulo limanena momveka bwino kuti Chilamulo, kuphatikizapo lamulo loti anayenera “kulandira zakhumi,” sichikugwira ntchito kwa Akhristu.​—Aheberi 7:​5, 18; Akolose 2:​13, 14.

 M’malo mopereka chakhumi ndiponso nsembe, a Mboni za Yehova amatsanzira chitsanzo cha Akhristu oyambirira, omwe ankachita zinthu ziwiri kuti utumiki wawo uziyenda bwino. Choyamba, iwo amagwira ntchito yolalikira popanda kulandira malipiro alionse. Chachiwiri, amapereka mwakufuna kwawo ndalama kapena chuma chawo kuti zithandizire pa ntchitoyi.

 Choncho timatsatira malangizo amene ali m’Baibulo, akuti: “Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.”​—2 Akorinto 9:7.