N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Amabwereranso Kunyumba za Anthu Omwe Anakana Kuti Awalalikire?
A Mboni za Yehova amalalikira anthu onse uthenga wa m’Baibulo chifukwa chakuti amakonda Mulungu komanso anthu ena. Amalalikiranso ngakhale anthu omwe nthawi ina anakana kuwalalikira. (Mateyu 22:37-39) Kukonda Mulungu kumatichititsa kuti tizimvera lamulo limene mwana wake anatiuza lakuti ‘tizipereka umboni wokwanira.’ (Machitidwe 10:42; 1 Yohane 5:3) Chifukwa chomvera lamulo limeneli, timalalikira anthu maulendo angapo ngatinso mmene aneneri akale a Mulungu ankachitira. (Yeremiya 25:4) Komanso chifukwa chakuti timakonda anzathu, timauza aliyense ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’ Timalalikira uthenga wa chipulumutsowu ngakhale kwa anthu omwe nthawi ina anakana kuti tiwalalikire.—Mateyu 24:14.
Nthawi zambiri timapeza anthu achidwi pakhomo lomwe poyamba anatiuza kuti sakufuna kuti tiwalalikire. Onani zifukwa zitatu zomwe zimachititsa zimenezi.
Anthu amasamuka.
Anthu ena pakhomo lomwelo amatha kukhala ndi chidwi ndi uthenga wathu.
Anthu amasintha. Zinthu zikasintha m’dzikoli komanso pamoyo wa munthu, zimachititsa munthu kuzindikira ‘zosowa zake zauzimu’ n’kufuna kuti aphunzire Baibulo. (Mateyu 5:3) Ngakhalenso anthu omwe amatitsutsa amatha kusintha ngati mmene anachitira mtumwi Paulo.—1 Timoteyo 1:13.
Komabe sitikakamiza anthu kuti amvetsere uthenga wathu. (1 Petulo 3:15) Timaona kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wosankha yekha zimene akufuna pa nkhani yolambira Mulungu.—Deuteronomo 30:19, 20.