N’chifukwa Chiyani Simugwiritsa Ntchito Mtanda Polambira?
Anthu ambiri amaona kuti mtanda ndi chizindikiro chimene Akhristu padziko lonse lapansi amagwiritsa ntchito. Ngakhale kuti ifenso a Mboni za Yehova ndi Akhristu, sitigwiritsa ntchito mtanda polambira. N’chifukwa chiyani zili choncho?
Chifukwa chimodzi n’chakuti Baibulo limasonyeza kuti Yesu sanafere pamtanda koma anafera pamtengo umodzi woongoka. Komanso Baibulo limachenjeza Akhristu mwamphamvu kuti “thawani kupembedza mafano,” omwe akuphatikizapo kugwiritsa ntchito mtanda polambira.—1 Akorinto 10:14; 1 Yohane 5:21.
Komanso n’zochititsa chidwi kuti Yesu anati: “Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yohane 13:34, 35) Zimene Yesu ananenazi zikuonetseratu kuti otsatira ake enieni adzadziwika ndi kusonyezana chikondi chenicheni, osati kugwiritsa ntchito mtanda kapena zizindikiro zina.