Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi Munthu Atafuna Angasiye Kukhala wa Mboni za Yehova?

Kodi Munthu Atafuna Angasiye Kukhala wa Mboni za Yehova?

 Ee. Munthu akhoza kusiya kukhala wa Mboni pogwiritsa ntchito njira ziwiri izi:

  •   Kupempha. Munthu akhoza kulemba kalata kapena kungonena kuti sakufunanso kukhala wa Mboni za Yehova.

  •   Zochita zake. Munthu angachite zinazake zomwe zingachititse kuti asakhalenso m’gulu lathu. (1 Petulo 5:9) Mwachitsanzo, munthuyo angalowe m’chipembedzo china n’kusonyeza kuti akufuna kupitiriza kukhala m’chipembedzocho.—1 Yohane 2:19.

Nanga bwanji ngati munthu wasiya kulalikira kapena kupita kumisonkhano yanu? Kodi mumamuona kuti wasiya kukhala wa Mboni?

 Ayi, si choncho. Kusankha kusiya kukhala wa Mboni za Yehova n’kosiyana kwambiri ndi kungofooka. Nthawi zambiri, anthu amene asiya kupita kumisonkhano kapena kulalikira sikuti amakhala kuti akufuna kusiya kukhala a Mboni. Amakhala kuti angofooka chifukwa chokhumudwa ndi zinazake. Choncho timayesetsa kulimbikitsa ndiponso kuthandiza anthu oterewa. (1 Atesalonika 5:14; Yuda 22) Ngati munthu wotereyu akufuna kuthandizidwa, akulu amumpingo amamuthandiza mwauzimu.—Agalatiya 6:1; 1 Petulo 5:1-3.

 Komabe udindo wa akulu si kukakamiza munthu kuti akhalebe wa Mboni za Yehova. Aliyense amasankha yekha pa nkhani ya chipembedzo. (Yoswa 24:15) Timakhulupirira kuti anthu ayenera kulambira Mulungu mwa kufuna kwawo komanso kuchokera mumtima.—Salimo 110:3; Mateyu 22:37.