Kodi a Mboni za Yehova Amapangitsa Kuti Mabanja a Anthu Athe Kapena Alimbe?
Ife a Mboni za Yehova timayesetsa kukhala ndi mabanja olimba komanso timathandiza anthu ena kuti akhale ndi mabanja olimba. Timadziwa kuti Mulungu ndi amene anayambitsa banja. (Genesis 2:21-24; Aefeso 3:14, 15) Kudzera m’Baibulo, Mulungu anapereka mfundo zimene zathandiza anthu padziko lonse kukhala ndi mabanja olimba komanso osangalala.
Mmene a Mboni za Yehova Amathandizira Kuti Mabanja Akhale Olimba
Timayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo chifukwa amatithandiza kuti tikhale amuna, akazi komanso makolo abwino. (Miyambo 31:10-31; Aefeso 5:22–6:4; 1 Timoteyo 5:8) Malangizo a m’Baibulo amathandiza ngakhale mabanja a anthu azipembedzo zosiyana kuti aziyenda bwino. (1 Petulo 3:1) Taonani zimene anthu ena omwe si Mboni ananena zokhudza amuna komanso akazi awo omwe ndi Mboni:
“Kwa zaka 6 kuchokera pamene tinakwatirana tinkangokhalira kukangana. Koma mkazi wanga dzina lake Ivete atakhala wa Mboni za Yehova, ankachita zinthu mwachikondi komanso moleza mtima kusiyana ndi kale. Zimenezi zinapangitsa kuti banja lathu lilimbe.”—Clauir, wa ku Brazil.
“Mwamuna wanga, Chansa, atayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova ndinkamuletsa chifukwa ndinkaganiza kuti a Mboni amathetsa mabanja a anthu. Koma ndaona kuti mwamuna wanga atangoyamba kuphunzira Baibulo, banja lathu linayamba kuyenda bwino kwambiri.”—Agness, wa ku Zambia.
Tikamalalikira, timasonyeza anthu mmene kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo kungawathandizire kuti
Kodi m’banja mumakhala mavuto munthu akasintha chipembedzo?
Nthawi zina amakhalapo. Mwachitsanzo, mu 1998 lipoti limene kampani ina yochita kafukufuku inapeza linanena kuti pa mabanja 20 alionse amene mmodzi anali wa Mboni za Yehova, banja limodzi linakumanapo ndi mavuto aakulu pa nthawi imene winayo anangoyamba kuphunzira ndi a Mboni.—Sofres
Yesu ananeneratu kuti anthu amene adzakhale otsatira ake, nthawi zina akhoza kutsutsidwa ndi anthu a m’banja mwawo. (Mateyu 10:32-36) Katswiri wina wa mbiri yakale dzina lake Will Durant, ananena kuti mu Ufumu wa Roma, “Chikhristu chinkagawanitsa mabanja,” a ndipo masiku ano, anthu enanso amanena kuti a Mboni za Yehova amagawanitsa mabanja. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti a Mboni ndi amene amapangitsa kuti mabanja azitha?
Poweruza pa mlandu wakuti a Mboni za Yehova amapangitsa kuti mabanja a anthu azitha, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linanena kuti anthu a m’banja la munthu amene ndi wa Mboni, nthawi zambiri amayambitsa mikangano chifukwa chokana “kuvomereza komanso kulemekeza ufulu wachipembedzo wa wachibale wawoyo wochita zinthu za kuchipembedzo chake.” Khotili linawonjezeranso kuti: “Mavuto amenewa amakhalapo m’mabanja onse amene anthu ndi osiyana zipembedzo osati m’mabanja a Mboni za Yehova okha.” b A Mboni za Yehova akamazunzidwa chifukwa cha chipembedzo chawo nthawi zonse amayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Musabwezere choipa pa choipa. . . . Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere.”—Aroma 12:17, 18.
N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova amakhulupirira kuti ayenera kukwatirana ndi anthu a m’chipembedzo chawo chokha?
A Mboni amatsatira lamulo la m’Baibulo loti munthu akwatire “mwa Ambuye,” zomwe zikutanthauza kukwatirana ndi munthu amene amakhulupirira zinthu zofanana ndi iwowo. (1 Akorinto 7:39) Lamulo limeneli ndi la m’Baibulo komanso ndi lothandiza kwambiri. Mwachitsanzo, nkhani imene inatuluka mu 2010 m’magazini ina inanena kuti, “anthu okwatirana akakhala kuti onse ndi a chipembedzo chimodzi,” amagwirizana kwambiri.—Journal of Marriage and Family. c
Komabe, a Mboni sauza anthu a m’chipembedzo chawo kuti athetse ukwati zikakhala kuti mwamuna kapena mkazi wawo si Mboni. Baibulo limati: “Ngati pali m’bale amene ali ndi mkazi wosakhulupirira, ndipo mkaziyo akulola kukhala naye, asamusiye mkaziyo. Ndiponso mkazi amene mwamuna wake ndi wosakhulupirira, koma mwamunayo akulola kukhala naye, asamusiye mwamuna wakeyo.”—1 Akorinto 7:12, 13. A Mboni za Yehova amatsatira lamulo limeneli.