Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sakondwerera Masiku Akubadwa?

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sakondwerera Masiku Akubadwa?

 A Mboni za Yehova sakondwerera nawo masiku akubadwa chifukwa amakhulupirira kuti Mulungu sasangalala ndi zikondwerero zimenezi. Ngakhale kuti Baibulo silifotokoza zambiri zokhudza kukondwerera masiku akubadwa, pali mfundo zotithandiza kudziwa zoyenera kuchita komanso kumvetsa mmene Mulungu amaonera zikondwerero zimenezi. Onani mfundo 4 zotsatirazi zomwe zikugwirizana ndi mfundo za m’Baibulo.

  1.   Zikondwerero zamasiku akubadwa zinayambitsidwa ndi zipembedzo zonyenga. Mogwirizana ndi dikishonale ina (Funk & Wagnalls Standard Dictionary of Folklore, Mythology, and Legend), zikondwerero zimenezi zinachokera ku chikhulupiriro chakuti tsiku limene munthu anabadwa, “mizimu yoipa ingathe kuvulaza munthu amene anabadwa patsikulo” ndipo “anzake omufunira zabwino akapezekapo, zimathandiza kuti munthuyo asavulazidwe ndi mizimu yoipayo.” Buku lina (The Lore of Birthdays) limanena kuti kalekale anthu ankagwiritsa ntchito zinthu zomwe zimachitika pa tsiku lobadwa kuti “ziwathandize kulosera zam’tsogolo pogwiritsa ntchito nyenyezi kapena mapulaneti” ndipo ankachita zimenezi potengera “mphamvu zinazake za sayansi yolosera zinthu popenda nyenyezi.” Bukuli limanenanso kuti “anthu amakhulupirira makandulo amene amayatsidwa pokondwererera tsiku lakubadwa kuti ali ndi mphamvu zamatsenga zothandiza munthu kupeza madalitso.”

     Komabe, Baibulo limaletsa kuchita zamatsenga, kulosera, kuchita zamizimu kapenanso kuchita chilichonse chokhudzana ndi zimenezi. (Deuteronomo 18:14; Agalatiya 5:19-21) Ndipotu chifukwa china chimene Mulungu ananenera kuti mzinda wakale wa Babulo udzawonongedwa, chinali chakuti anthu amumzindawo ankakhulupirira nyenyezi imenenso ndi njira ina yolosera zam’tsogolo. (Yesaya 47:11-15) M’malo motanganidwa ndi kufufuza mmene mwambo uliwonse unayambira, a Mboni za Yehova amadalira kwambiri malangizo a m’Baibulo omwe akugwirizana ndi nkhaniyo posankha zochita.

  2.   Akhristu oyambirira sankakondwerera masiku akubadwa. Buku lina (The World Book Encyclopedia) limanena kuti “iwo ankaona kuti kukondwerera masiku akubadwa n’kogwirizana ndi miyambo ya zipembedzo zonyenga.” Baibulo limafotokoza kuti atumwi komanso anthu ena amene anaphunzitsidwa ndi Yesu anapereka chitsanzo chimene Akhristu ena onse ayenera kutsatira.​—2 Atesalonika 3:6.

  3.   Akhristu amaona kuti mwambo wokhawo umene ayenera kumachita ndi kukumbukira imfa ya munthu osati kubadwa kwake. Mwachitsanzo, iwo amakumbukira imfa ya Yesu. (Luka 22:17-​20) Zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa Baibulo limanena kuti “tsiku lomwalira limaposa tsiku lobadwa.” (Mlaliki 7:1) Pofika kumapeto a moyo wake wapadziko lapansi, Yesu anali atapanga dzina labwino kwa Mulungu, ndipo zimenezi zinachititsa kuti tsiku lake lomwalira likhale lofunikira kwambiri kuposa tsiku lake lobadwa.​—Aheberi 1:4.

  4.   Baibulo silitchula nkhani ina iliyonse yokhudza mtumiki wa Mulungu amene anakondwererapo tsiku lakubadwa. Koma sikuti anaiwala kulembamo zokhudza masiku akubadwa. Baibulo limangotchula zikondwerero ziwiri zokha zomwe anachita ndi anthu amene sankatumikira Mulungu. Koma pa zikondwerero ziwirizi panachitika zoipa.​—Genesis 40:20-22; Maliko 6:21-29.

Kodi ana amene makolo awo ndi Mboni za Yehova amaona kuti akumanidwa zinazake chifukwa choti sakondwerera masiku akubadwa?

 Mofanana ndi makolo ena onse amene amafunira ana awo zabwino, a Mboni za Yehova amakonda ana awo nthawi ina iliyonse. Amachita zimenezi powapatsa mphatso ndiponso kuwatengera kumalo osiyanasiyana kuti akasangalale. Iwo amayesetsa kutengera chitsanzo cha Mulungu yemwe amapereka zinthu zabwino kwa ana ake mowolowa manja. (Mateyu 7:11) Ana omwe makolo awo ndi a Mboni za Yehova samaona kuti akumanidwa zinazake. Onani zimene ana ena ananena:

  •   “Zimasangalatsa kwambiri kulandira mphatso pa nthawi imene sumaiyembekezera.”​—Tammy, wazaka 12.

  •   “Ngakhale kuti makolo anga samandigulira mphatso pa tsiku lomwe ndinabadwa, komabe amandigulira mphatso nthawi ina iliyonse. Ndimasangalala kulandira mphatso pa nthawi imene sindimaiyembekezera.”​—Gregory, wazaka 11.

  •   “Kodi mukuona kuti munthu anganjoye kwa 10 minitsi akangodya makeke kapenanso kumvetsera nyimbo basi? Mubwere kwathu mudzaone mmene ife timanjoyera.”​—Eric, wazaka 6.