Kodi a Mboni Amafuna Kuti Ndikamaphunzira Nawo Baibulo Nanenso Ndikhale wa Mboni?
Ayi, imeneyi si nkhani yokakamiza ngakhale pang’ono. Anthu ambiri amasangalala kuphunzira nafe Baibulo osati ndi cholinga choti alowe mpingo wathu. a Timaphunzira Baibulo ndi anthu pofuna kuwauzako zimene Baibulo limaphunzitsa. Inuyo mumasankha nokha kugwiritsa ntchito zimene mukuphunzirazo. Timadziwa kuti munthu aliyense ayenera kusankha yekha kuti azikhulupirira Mulungu kapena ayi.—Yoswa 24:15.
Kodi n’zotheka kumagwiritsa ntchito Baibulo langa pophunzira?
Inde. Muli ndi ufulu wogwiritsa ntchito Baibulo lanu, ngakhale kuti ife timakonda kugwiritsa ntchito Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lomwe ndi losavuta kumva ndipo tingathe kukugawirani ngati mutalifuna. Mungathe kupeza uthenga wokhudza chiyembekezo cha anthu komanso wopatsa chipulumutso pafupifupi m’Baibulo lililonse.
Nanga n’chifukwa chiyani mumaphunzira ndi anthu oti sangalowe m’chipembedzo chanu?
-
Chifukwa chachikulu ndi chakuti timakonda Mulungu yemwe amafuna kuti Akhristu aziphunzitsa ena zimene iwo amaphunzira. (Mat. 22:37, 38; 28:19, 20) Choncho ife timaona kuti ndi mwayi waukulu kukhala “antchito anzake a Mulungu” pothandiza anthu kuti adziwe zimene Mawu ake amaphunzitsa.—1 Akorinto 3:6-9.
-
Timachitanso zimenezi chifukwa timakonda anthu. (Mateyu 22:39) Ndipotu timasangalala kwambiri kuuzako ena zinthu zosangalatsa zimene taphunzira.—Machitidwe 20:35.
a Kusonyeza kukula kwa ntchito yathu yophunzitsa anthu Baibulo, mu 2023 tinkaphunzira Baibulo ndi anthu okwana 7,281,212 mwezi uliwonse. Ndipo nthawi zambiri tinkaphunzira ndi anthu ochuluka nthawi imodzi. Koma anthu 269,517 okha ndi amene anabatizidwa n’kukhala a Mboni za Yehova chaka chimenechi.