Kodi Mumalandira Chithandizo cha Kuchipatala?
Inde, ife a Mboni za Yehova timalandira chithandiza chakuchipatala. Ngakhale kuti timayesetsa kudzisamalira kuti tikhale ndi thanzi labwino, nthawi zina ‘timafunikabe dokotala.’ (Luka 5:31) Ndipotu anthu ena a Mboni za Yehova ndi madokotala, mofanana ndi mmene Luka wa m’nthawi ya atumwi analili.—Akolose 4:14.
Komabe, pali zithandizo zina za kuchipatala zimene zimatsutsana ndi mfundo za m’Baibulo ndipo ife timakana zithandizo zoterozo. Mwachitsanzo, timakana kuikidwa magazi chifukwa Baibulo limaletsa. (Machitidwe 15:20) Komanso Baibulo limaletsa njira iliyonse yothandizira odwala imene imagwirizana ndi zamizimu.—Agalatiya 5:19-21.
Komabe, zithandizo zambiri zakuchipatala n’zosatsutsana ndi mfundo za m’Baibulo ndipo munthu amafunika kusankha yekha chochita pa nkhani zoterezi. Mwachitsanzo, munthu wina wa Mboni angasankhe kulandira mankhwala enaake kapena chithandizo chinachake. Koma munthu winanso wa Mboni angakane kulandira zinthu zomwezo.—Agalatiya 6:5.