Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi Chipembedzo cha Mboni za Yehova ndi cha Chipulotesitanti?

Kodi Chipembedzo cha Mboni za Yehova ndi cha Chipulotesitanti?

 Ayi. Ife a Mboni za Yehova ndife Akhristu koma chipembedzo chathu si cha Chipulotesitanti. N’chifukwa chiyani tikutero?

 Zipembedzo za Chipulotesitanti ndi zomwe “zimatsutsa chipembedzo cha Roma Katolika.” Ngakhale kuti ife a Mboni za Yehova sitigwirizana ndi zimene tchalitchi cha Katolika chimaphunzitsa, timaona kuti sitili m’gulu la zipembedzo za Chipulotesitanti pa zifukwa zotsatirazi:

  1.   Zinthu zambiri zimene anthu a zipembedzo za Chipulotesitanti amakhulupirira sizigwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Mwachitsanzo, Baibulo limaphunzitsa kuti “pali Mulungu mmodzi,” osati milungu itatu mwa Mulungu m’modzi. (1 Timoteyo 2:5; Yohane 14:28) Baibulo limanenanso momveka bwino kuti Mulungu amalanga anthu oipa, osati powawotcha kumoto, koma ndi “chiwonongeko chamuyaya.”​—Salimo 37:9; 2 Atesalonika 1:9.

  2.   Sitiumiriza tchalitchi cha Katolika kapena tchalitchi chilichonse kuti chisinthe zimene chimakhulupirira. M’malomwake, timangolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu n’kumathandiza ena kuti azikhulupirira zimene uthenga wabwinowo umanena. (Mateyu 24:14; 28:​19, 20) Ife cholinga chathu sikusintha zimene zipembedzo zina zimakhulupirira koma kuphunzitsa munthu aliyense payekha amene akufuna kuti adziwe zoona zenizeni zimene Mawu a Mulungu amanena.​​—Akolose 1:​9, 10; 2 Timoteyo 2:​24, 25.