Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi a Mboni za Yehova Amaona Bwanji Sayansi?

Kodi a Mboni za Yehova Amaona Bwanji Sayansi?

 Timalemekeza zinthu zimene zatheka chifukwa cha sayansi ndipo timakhulupirira zimene a sayansi anapeza zomwe zili ndi umboni.

 Malinga ndi dikishonale ina yotchedwa Collins Cobuild Advanced Learner’s English Dictionary, mawu oti sayansi amatanthauza “kuphunzira zinthu za m’chilengedwe ndi mmene zimachitira zinthu komanso nzeru zimene timapeza kuchokera ku zinthuzo.” Ngakhale kuti Baibulo si buku la sayansi, limalimbikitsa anthu kuti aziphunzira za zinthu za m’chilengedwe komanso kupindula ndi zimene asayansi ena apeza. Taonani zitsanzo izi:

  •   Sayansi ya Zakuthambo: “Kwezani maso anu kumwamba muone. Kodi ndani amene analenga zinthu zimenezo? Ndi amene akutsogolera gulu lonse la nyenyezizo malinga ndi chiwerengero chake, ndipo amaziitana potchula iliyonse dzina lake.”—Yesaya 40:26.

  •   Sayansi ya Zinthu Zamoyo: Solomo “ankafotokoza za mitengo, kuyambira mkungudza wa ku Lebanoni mpaka kamtengo ka hisope kamene kamamera pakhoma. Ankafotokozanso za zinyama, zolengedwa zouluka, nsomba, ndiponso za zokwawa.”—1 Mafumu 4:33.

  •   Zamankhwala: “Anthu athanzi safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.”—Luka 5:31.

  •   Zanyengo: “Kodi unalowapo munkhokwe ya chipale chofewa, Kapena umaziona nkhokwe za matalala. . . ? Ndiponso njira imene mphepo ya kum’mawa imamwazikira padziko lapansi ili kuti?”—Yobu 38:22-24.

 Mabuku athu amalemekeza sayansi chifukwa amakhala ndi nkhani zokhudza chilengedwe komanso zinthu zimene zatheka chifukwa cha sayansi. Makolo omwe ndi a Mboni alimbikitsa ana awo kuti azipita ku sukulu n’cholinga choti aphunzire zinthu zambiri. A Mboni za Yehova ena amagwira ntchito zokhudza sayansi, monga zimene zimachitika m’maselo a zinthu zamoyo, masamu, komanso sayansi ya mphamvu za m’chilengedwe.

Zimene sayansi singakwanitse

 Sitikhulupirira kuti sayansi ingathandize anthu kupeza mayankho a mafunso awo onse. a Mwachitsanzo, akatswiri asayansi ya za m’nthaka amafufuza zinthu zimene zimapanga dziko lapansi. Akatswiri asayansi ya zinthu zamoyo amaphunzira mmene thupi limagwirira ntchito. Koma kodi n’chifukwa chiyani dzikoli lili malo abwino kwambiri okhala zinthu zamoyo? Nanga n’chifukwa chiyani ziwalo zosiyanasiyana za m’thupi zimagwira ntchito mogwirizana?

 Timaona kuti ndi Baibulo lokha limene limapereka mayankho ogwira mtima a mafunso amenewa. (Salimo 139:13-16; Yesaya 45:18) Choncho, timakhulupirira kuti munthu ayenera kuphunzira zokhudza sayansi komanso Baibulo kuti akhale ndi maphunziro abwino.

 Nthawi zina sayansi ingaoneke ngati ikutsutsa zimene Baibulo limanena. Komabe, zimenezi zimachitika chifukwa chosamvetsa bwino zimene Baibulo kwenikweni limaphunzitsa. Mwachitsanzo, Baibulo siliphunzitsa kuti dzikoli linalengedwa m’masiku 6 okhala ndi maola 24.—Genesis 1:1; 2:4.

 Mfundo zina zimene anthu ena amaganiza kuti n’zogwirizana ndi sayansi, zimakhala zopanda umboni wokwanira ndipo akatswiri ena asayansi odziwika bwino sagwirizana ndi mfundo zoterezi. Mwachitsanzo, chifukwa choti zinthu za m’chilengedwe zimasonyeza kuti pali winawake wanzeru amene anazipanga, timagwirizana ndi asayansi komanso anthu ena amene amakhulupirira kuti zamoyo sizinachite kusintha kuchokera ku zinthu zopanda moyo.

a Katswiri wa sayansi ya mphamvu za m’chilengedwe wa ku Austria, dzina lake Erwin Schrödinger, analemba kuti sayansi “sifotokoza zonse pa zinthu . . . zimene timaziganizira kwambiri komanso zinthu zimene timaziona kuti n’zofunika.” Komanso Albert Einstein ananena kuti: “Zimene takumana nazo pamoyo, zatiphunzitsa m’njira yopweteka kuti kungokhala munthu woganiza bwino sikungathandize munthu kuthana ndi mavuto a tsiku ndi tsiku.”