N’chifukwa Chiyani Simukondwerera Isitala?
Maganizo olakwika amene anthu ena amakhala nawo
Zimene ena amanena: A Mboni za Yehova sakondwerera Isitala chifukwa iwowo si Akhristu.
Zoona zake: Timakhulupirira kuti Yesu Khristu ndi Mpulumutsi wathu ndipo timayesetsa ‘kutsatira mapazi ake mosamala kwambiri.’—1 Petulo 2:21; Luka 2:11.
Zimene ena amanena: Simukhulupirira zoti Yesu anaukitsidwa.
Zoona zake: Timakhulupirira zoti Yesu anaukitsidwa. Timazindikiranso kuti chikhulupiriro chachikhristu chagona pa mfundo yakuti Yesu anaukitsidwa ndipo timauza ena zimenezi tikamalalikira.—1 Akorinto 15:3, 4, 12-15.
Zimene ena amanena: Sizikukhudzani kuti ana anu amasirira anzawo akamasangalala pa holide ya Isitala.
Zoona zake: Timakonda ana athu ndipo timachita khama kwambiri powaphunzitsa ndi kuwathandiza kuti azisangalala.—Tito 2:4.
N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova sakondwerera Isitala?
Chikondwerero cha pa Isitala n’chosagwirizana ndi Baibulo.
Yesu anatilamula kuti tizikumbukira imfa yake, osati kuukitsidwa kwake. Timakumbukira imfa imeneyi chaka chilichonse pa tsiku limene Yesuyo anaphedwa, mogwirizana ndi kalendala yotchulidwa m’Baibulo.—Luka 22:19, 20.
Timakhulupirira kuti Mulungu sasangalala ndi miyambo ya pa Isitala chifukwa inachokera kumiyambo yakale yokhudzana ndi kulambira milungu imene anthu ankakhulupirira kuti ili ndi mphamvu zobereketsa. Mulungu amafuna kuti anthu ‘azidzipereka kwa iye yekha,’ ndipo amakhumudwa anthu akamachita miyambo imene iye sasangalala nayo.—Ekisodo 20:5; 1 Mafumu 18:21.
Timakhulupirira kuti zimene tinasankha zoti tisamakondwerere nawo Isitala n’zogwirizana kwambiri ndi Baibulo, lomwe limatilimbikitsa kuti tizigwiritsa ntchito “nzeru zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino” m’malo mongotsatira miyambo ya anthu. (Miyambo 3:21; Mateyu 15:3) Anthu ena akatifunsa zimene timakhulupirira pa nkhani ya Isitala, timawauza. Komabe, timalemekeza zimene munthu aliyense wasankha kuti azikhulupirira pa nkhaniyi.—1 Petulo 3:15.