Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi Bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society Ndi Chiyani?

Kodi Bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society Ndi Chiyani?

 Bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania linakhazikitsidwa mu 1884 motsatira malamulo a ku Pennsylvania m’dziko la United States ndipo cholinga chake si kupeza ndalama. A Mboni za Yehova amagwiritsa ntchito bungweli pochita zinthu monga kufalitsa Mabaibulo ndiponso mabuku ena.

 Zolinga za bungweli n’zokhudza “chipembedzo, maphunziro ndiponso kuthandiza anthu.” Koma cholinga chake chachikulu ndi “kulalikira ndiponso kuphunzitsa uthenga wa Ufumu wa Mulungu womwe Mfumu yake ndi Yesu Khristu.” Kuti munthu akhale m’bungweli amachita kupemphedwa ndipo sizidalira ndalama zimene munthuyo amapereka. Anthu amene ali m’bungweli amathandiza Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova.

Mabungwe Enanso

 Kuwonjezera pa bungweli, a Mboni za Yehova amagwiritsanso ntchito mabungwe ena m’mayiko osiyanasiyana. Ena mwa mabungwewa ndi akuti, “Watch Tower” kapena “Watchtower.”

 Mabungwewa akhala akuthandiza Mboni za Yehova pa ntchito zotsatirazi:

  •   Kulemba ndi kufalitsa mabuku. Tafalitsa Mabaibulo pafupifupi 220 miliyoni ndiponso mabuku ena pafupifupi 40 biliyoni m’zilankhulo zoposa 700. Pawebusaiti yathu ya jw.org munthu akhoza kuwerenga Baibulo m’zilankhulo zoposa 120 popanda kulipira. Akhozanso kupeza mayankho a mafunso monga “Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

  •   Maphunziro. Timakhala ndi sukulu zosiyanasiyana zophunzitsa Baibulo. Mwachitsanzo, kuyambira mu 1943, a Mboni za Yehova oposa 8,000 amaliza maphunziro a Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo ndipo apita kukakhala amishonale kapena kukathandiza pa ntchito yolalikira kumayiko ena. Mlungu uliwonse anthu ambiri, ngakhalenso amene si Mboni, amaphunzitsidwanso pamisonkhano ya kumipingo yathu. Timakhalanso ndi sukulu zophunzitsa anthu kuwerenga ndi kulemba ndipo buku limene limagwiritsidwa ntchito pa sukuluyi lafalitsidwa m’zilankhulo 110.

  •   Kuthandiza anthu. Timapereka chithandizo kwa anthu amene akumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, tinathandiza anthu pa nthawi ya nkhondo imene inachitika ku Rwanda mu 1994 komanso pa nthawi ya chivomezi chimene chinachitika ku Haiti mu 2010.

 Ngakhale kuti timachita zinthu zambiri pogwiritsa ntchito mabungwewa, sikuti timawadalira kuti tizigwira ntchito yathu yolalikira. Mkhristu aliyense ali ndi udindo wotsatira lamulo limene Mulungu anapereka lakuti tizilalikira ndiponso kuphunzitsa uthenga wabwino. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Timakhulupirira kuti Mulungu amathandiza ntchito yathuyi ndipo adzapitirizabe ‘kuikulitsa.’—1 Akorinto 3:6, 7.