Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Tisamuke Pasanathe Masiku 60!

Tisamuke Pasanathe Masiku 60!

Lachisanu pa July 5, 2013 anthu a ku Beteli ya ku United States, anasangalala ndi chilengezo chimene Anthony Morris wa m’Bungwe Lolamulira analengeza. Chilengezocho chinali chakuti: “Tagwirizana kuti tigulitse nyumba zokwana 6. Nyumbazi zili ku 117 Adams Street ndi ku 90 Sands Street m’dera la Brooklyn. * Kuti zitheke kugulitsa nyumba 5, tifunika tisamukemo pofika mkatikati mwa mwezi wa August chaka chino.”

Zimenezi zinaonetseratu kuti pakhala ntchito yaikulu. Izi zili choncho chifukwa chakuti malo onse a mkati mwa nyumbazi kukula kwake n’kofanana ndi mabwalo a mpira wa miyendo okwana 11. Koma tikufunika kusamuka m’nyumbazi m’masiku 60 okha basi.

Kwa zaka zambiri m’nyumba zokwanira 5 zimenezi, munali makina osindikizira mabuku, koma m’chaka cha 2004 makinawa anawasamutsira ku Wallkill, m’dera la New York.

Kungoyambira nthawi imeneyi, m’nyumbazi anayamba kusungamo katundu komanso kukonzeramo zinthu zowonongeka. Katundu yemwe wakhala akusungidwa m’nyumbazi ndi monga womangira, mipando ndi matebulo za m’maofesi ndiponso katundu wothandiza pa ntchito ya zomangamanga ku United States komanso ndi kumayiko ena.

Pofuna kuti tisamuke pa nthawi yake komanso kuti ntchito yosamukayi iyende bwino, panafunika kuchita zinthu mosamala. Choyamba, panafunika kulemba katundu yense amene anali m’nyumbazi kuti zidziwike ngati katundu wina angagulitsidwe kusungidwa kapena kutayidwa. Chachiwiri, panakonzedwa zoti ntchitoyi ichitike mwachangu komanso mopewa ngozi.

Anthu onse a pa Beteli anathandiza nawo pa ntchitoyi. Kuonjezera pamenepa, anthu enanso okwana 41 ongodzipereka ochokera m’madera osiyanasiyana a dziko la United States, anabwera ku Beteli kudzathandiza ntchitoyi. Ambiri anali anyamata amphamvu osakwatira. Anyamatawa anavomera kudzatumikira kuyambira pa masabata 6 mpaka 10. Iwo analolera kusiya achibale awo, anzawo ndiponso ntchito, n’cholinga chokatumikira ku Beteli. Kodi anamva bwanji atapemphedwa kuchita utumiki umenewu?

Jordan, yemwe ali ndi zaka 21, anachokera m’dera la Washington, ndipo ananena kuti: “Ndinachita bwino kupereka fomu yopempha kuchita nawo utumiki umenewu.”

Mnyamata wina zaka 20 dzina lake Steven, anachokera m’dera la Texas. Iye ananena kuti: “Ndikuona kuti ndili m’banja lalikulu, losangalala komanso lakhama pogwira ntchito.”

Mnyamata winanso wa zaka 23 dzina lake Justin, analemba kuti: “Kuno ku Beteli kumangokhala ngati kwathu. Ndimasangalala kwambiri chifukwa ndimatumikira ndi abale komanso alongo amene amakonda zinthu zauzimu komanso amakondana.”

Mnyamata wina wa zaka 20 dzina lake Adler, anachokera kudziko la Puerto Rico. Iye ananena kuti: “Ndimavutika kudzuka m’mawa kwambiri, komabe ndikusangalala chifukwa utumikiwu wandithandiza kupeza anzanga odalirika.”

William, yemwe ali ndi zaka 21 ananena kuti: “Kuyambira ndili mwana ndakhala ndikulakalaka kudzatumikira ku Beteli. Koma atandiitana kuti ndidzathandize pa ntchitoyi ndinkaganiza, ndinayamba kuganiza kuti ndidzasowa anzanga ocheza nawo, koma ndaona kuti maganizo amenewa anali olakwika.”

Kodi gulu la ogwira ntchito amenewa linamaliza kusamuka pamasiku amene anakonza? Inde, anakwanitsa kusamuka m’masiku 55 okha basi.

^ ndime 2 Tidzasamuka m’nyumba ya ku 90 Sands Street, m’chaka cha 2017.