Ntchito Yathu Yofalitsa Mabuku ndi Zinthu Zina

“Wokonzeka Mokwanira Kugwira Ntchito Iliyonse Yabwino”

Baibulo la Dziko Latsopano ndi losavuta kuwerenga komanso linamasulira mawu a chinenero choyambirira molondola. M’Baibuloli muli mapu amitundu yosiyanasiyana, matanthauzo a mawu ena a m’Baibulo ndi zakumapeto.

“Wokonzeka Mokwanira Kugwira Ntchito Iliyonse Yabwino”

Baibulo la Dziko Latsopano ndi losavuta kuwerenga komanso linamasulira mawu a chinenero choyambirira molondola. M’Baibuloli muli mapu amitundu yosiyanasiyana, matanthauzo a mawu ena a m’Baibulo ndi zakumapeto.

Baibulo la Dziko Latsopano Lokonzedwanso Linatulutsidwa M’Chisipanishi

Kodi omasulira Baibulo anakwanitsa bwanji kumasulira Baibulo limene mawu amodzi amatanthauza zinthu zingapo m’madera ena apadziko lapansi?

Mawu a Mulungu Ayamba Kuwafika Pamtima

Buku la Mateyu linatulutsidwa m’Chinenero Chamanja cha ku Japan. Onani mmene kukhala ndi Baibulo m’chinenero chimene munthu amamva bwino kulili kwa mtengo wapatali.

Ntchito Yomasulira M’chinenero Chamanja

A Mboni za Yehova amasulira mabuku ndi zinthu zina zofotokoza Baibulo m’zinenero zamanja zoposa 90. N’chifukwa chiyani amachita khama lonseli?

“Mavidiyowa Ndi Abwino Kwambiri Kuposa Mafilimu Ambiri”

Kodi anthu amanena zotani akaonera mavidiyo a Mboni za Yehova pamisonkhano yachigawo yomwe amakhala nayo chaka chilichonse? Kodi zimatheka bwanji kuti mavidiyowa akhale m’zilankhulo zosiyanasiyana?

Ntchito Yomasulira M’chinenero cha Manja cha ku Quebec Yathandiza Anthu Ambiri

N’chifukwa chiyani ntchito yomasulira m’chinenero chamanja ili yofunika?

Kuthandiza Anthu Kukonda Komanso Kulemekeza Choonadi

Aliyense amene amawerenga mabuku athu kapena kuonera mavidiyo athu amaona yekha kuti nkhani zake ndi zolondola komanso zofufuzidwa bwino.

Ntchito Yotumiza Mabuku ku Congo

A Mboni za Yehova amayenda mtunda wautali mwezi uliwonse kuti akasiye Mabaibulo ndiponso mabuku kwa anthu a m’dziko la Congo.

Dziko la Estonia Linayamikira Kwambiri Baibulo la Dziko Latsopano

M’chaka cha 2014, dziko la Estonia linaika Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika m’gulu la zinthu zomwe zinalembedwa bwino kwambiri m’chaka chimenecho.

Baibulo Longomvetsera Lokhala ndi owerenga Ambirimbiri

Anthu osiyanasiyana awerenga nawo Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso lomwe linatulutsidwa mu 2013, kuti likhale longomvetsera.

Zithunzi Zothandiza Kuti Nkhani Zikhale Zosangalatsa

Kodi ojambula zithunzi amatani kuti zithunzi zake zithandize kuti nkhani za m’mabuku athu zikhale zosangalatsa?

Mavidiyo a M’zinenero Zambiri

Vidiyo yakuti Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? ikupezeka m’zinenero pafupifupi 400, ndipo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo ikupezekanso m’zinenero zoposa 550. Mukhoza kuwapeza a m’chinenero chanu.

Kupanga Baibulo Latsopano

Onerani vidiyoyi kuti mudziwe zimene zinachitika pokonza Baibulo la Dziko Latsopano la chingelezi la 2013. N’chifukwa chiyani analola kuononga nthawi ndi ndalama zambiri kuti atulutse Baibulo latsopano lokongolali?

Ntchito Yomasulira Mabuku ku Mexico ndi ku Central America

N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova akumasulira mabuku othandiza pophunzira Baibulo ku Mexico ndi ku Central America m’zinenero zoposa 60 monga Chimaya, Chinawato ndi m’chinenero cha kumpoto kwa Germany?

Kuthandiza Anthu Amene Ali ndi Vuto Losaona, ku Africa

Anthu omwe ali ndi vuto losaona ku Malawi akuyamikira Yehova chifukwa cholandira mabuku ophunzirira Baibulo a zilembo zawo m’Chichewa.

Baibulo Lolimba Kwambiri

Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, lomwe linatulutsidwa mu 2013, ndi lolimba komanso lokongola kwambiri.

Gulu la Anthu Omasulira Chisipanishi Lasamukira ku Spain

Kuyambira mu 1907, mabuku othandiza anthu kumvetsa Baibulo ofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova anayamba kumasuliridwa m’Chisipanishi. Werengani zokhudza ntchito yomasulira mabuku awo m’Chisipanishi.

Mavidiyo Amene Amasangalatsa Mitima Yathu

A Mboni za Yehova amatulutsa mavidiyo a makatuni amene amaphunzitsa ana makhalidwe abwino komanso mfundo za m’Baibulo. Kodi mavidiyowa akhudza bwanji anthu?

Zaka 100 Tikuimba Nyimbo Zotamanda Mulungu

Kodi a Mboni za Yehova agwiritsa ntchito bwanji nyimbo polambira Mulungu?

Tapatsidwa Ntchito Yomasulira “Mawu Opatulika a Mulungu”​—Aroma 3:2

Kwa zaka zambiri, a Mboni za Yehova akhala akugwiritsira ntchito Mabaibulo osiyanasiyana. Koma n’chifukwa chiyani anaganiza zomasulira Baibulo m’Chingelezi chimene anthu amalankhula masiku ano?

Laibulale ya M’thumba

Laibulale ya JW ndi pulogalamu yaulere yomwe mungaike muzipangizo za m’manja ndipo ingakuthandizeni pophunzira Baibulo mozama.

Ntchito Yosindikiza Mabuku Ikuthandiza Anthu Padziko Lonse Kuphunzira za Mulungu

A Mboni za Yehova amasindikiza mabuku m’malo 15 padziko lonse, ndipo amasindikiza mabuku othandiza pophunzira Baibulo m’zinenero 700.

Webusaiti ya jw.org Tsopano Ili M’zinenero Zoposa 300!

Kodi a Mboni za Yehova amatha bwanji kumasulira uthenga wa m’Baibulo m’zinenero zambirimbiri? Kodi mawebusaiti ena odziwika bwino akupezeka m’zinenero zingati?

Nsanja ya Olonda ya M’chingerezi Chosavuta Kumva Ikuthandiza Pophunzitsa Ana ku Denmark

Onerani kavidiyoka kuti mudziwe mmene banja la ku Denmark limagwiritsira ntchito Nsanja ya Olonda ya m’chingerezi chosavuta kumva

“Njira ndi Iyi”

Mvetserani nyimbo, yotengedwa m’mavesi a M’mawu a Mulungu, yomwe yaimbidwa m’zinenero 8.

Kavidiyo: Nsanja ya Olonda ya M’Chingelezi Chosavuta Kumva Ikuthandiza Pophunzitsa Ana

Onerani kavidiyoka kuti mudziwe mmene banja lina limagwiritsira ntchito magazini ya Nsanja ya Olonda ya m’Chingelezi chosavuta kumva pophunzitsa ana awo za Mulungu.

Timavidiyo: “Ndikuthokoza Yehova Chifukwa Chondithandiza”

Onerani kavidiyoka kuti mudziwe mmene Nsanja ya Olonda ya m’Chingelezi chosavuta kumva yathandizira munthu wina kuti akhale pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova Mulungu.

Kavidiyo: “Kaya Ndikanagwira Mtengo Wanji?”

Onerani kavidiyoka kuti mumve zimene munthu wina wakhungu ananena poyamikira mmene Baibulo la zilembo za akhungu lamuthandizira.

Makina Ogometsa

Onani mmene makina ogometsawa amasindikizira mabuku, kuwadula, kuwasanja, kuwawerenga ndiponso kuwalongedza.

Amabwera Kudzaimba Nyimbo

Kwa zaka zoposa 40, anthu oimba ochokera m’madera osiyanasiyana padziko lapansili akhala akusangalala ndi mwayi wokhala m’gulu lapadera loimba nyimbo.

Kabuku ka M’zinenero Zosiyanasiyana ka Zithunzi Zophunzitsa

Kabuku ka Mverani Mulungu kathandiza anthu ambirimbiri padziko lonse kuti adziwe Mulungu komanso uthenga wa m’Baibulo. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene ena anena zokhudza kabukuka.

Nsanja ya Olonda ya M’Chigirinilandi Inayamikiridwa pa TV

Mu January 2013, pa pulogalamu ina ya pa TV anaulutsa kuti a Mboni za Yehova akhala akufalitsa magazini ya Nsanja ya Olonda ya m’Chigirinilandi kwa zaka 40.

Kugwiritsa Ntchito Zithunzi Pothandiza Anthu Owerenga Mabuku Athu

Mabuku ambiri a Mboni za Yehova amakhala ndi zithunzi zokongola zimene zimafotokozera nkhani. Komatu m’mbuyomu zimenezi sizinkachitika.

Anthu Akupatsidwa Mabaibulo a M’zinenero Zawo

Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika likuperekedwa mwaulere kwa aliyense amene akufuna kuliwerenga.

Buku la Genesis Tsopano Likupezeka M’Chinenero Chamanja cha ku America

Buku la Genesis tsopano likupezeka m’Chinenero Chamanja cha ku America

Ofesi ya Mboni za Yehova ku Japan Ikusindikiza Mabaibulo a Zikuto Zolimba Omwe Akutumizidwa M’madera Osiyanasiyana Padziko Lapansili

A Mboni za Yehova aika makina okonzera mabuku kufakitale yawo ya ku Japan. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zambiri zokhudza makina amenewa.

Masamba Achepa Koma Zinenero Zachuluka

Kuyambira mu January 2013, masamba a magazini iliyonse ya Galamukani! komanso Nsanja ya Olonda yogawira anachepetsedwa kuchoka pa 32 kufika pa 16. N’chifukwa chiyani anachepetsa chonchi?

Chibaibulo Chachikulu Kwambiri

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene zimachitika kuti tizifalitsa Mabaibulo a zilembo za akhungu m’zinenero zambiri.

Nsanja ya Olonda ya M’Chingelezi Chosavuta Kumva

Tinayamba kutulutsa Nsanja ya Olonda ya m’Chingelezi chosavuta kumva m’chaka cha 2011. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mmene magaziniyi ikuthandizira anthu padziko lonse lapansi.

Nsanja ya Olonda—Magazini Oposa Magazini Ena Onse

Timafalitsa ndiponso kugawira magazini a Nsanja ya Olonda padziko lonse m’zinenero zoposa 190. Kodi pali magazini ena amene akufalitsidwa kwambiri ngati magazini amenewa?