Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

“Wokonzeka Mokwanira Kugwira Ntchito Iliyonse Yabwino”

Kutulutsidwa kwa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika Lokonzedwanso

“Wokonzeka Mokwanira Kugwira Ntchito Iliyonse Yabwino”

Pa 18 August 2023, anthu okwana 77,112 anasonkhana m’madera okwana 20, pamene M’bale Kenneth Cook, Jr., wa m’Bungwe Lolamulira, anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lokonzedwanso m’Chichewa.

A Mboni za Yehova omwe amalankhula Chichewa analandira Baibulo la Dziko Latsopano lathunthu m’chinenero chawo koyamba mu 2010. a Mabaibulo a Dziko Latsopano okwana 1,046,382 asindikizidwa m’Chichewa ndipo a Mboni za Yehova oposa 138,000 omwe amalankhula Chichewa akhala akugwiritsa ntchito Baibulo limeneli kulikonse komwe ali. Koma n’chifukwa chiyani Baibuloli lakonzedwanso? Ndi ndani amene anagwira ntchito yokonza Baibuloli? Nanga tingatsimikizire bwanji kuti Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso ndi lodalirika? Kodi ndi zinthu ziti zimene awonjezeramo kuti zikuthandizeni kukhala “wokonzeka mokwanira kugwira ntchito iliyonse yabwino”?​—2 Timoteyo 3:16, 17.

N’chifukwa chiyani Baibuloli lakonzedwanso?

Popeza kuti chilankhulo chimasintha zaka zikamapita, pamafunika kukonzanso Mabaibulo n’cholinga choti mawu ake apitirizebe kumveka bwino. Ndi anthu ochepa chabe amene angapindule ndi Baibulo lomasuliridwa ndi mawu achikale.

Poyamba, Yehova Mulungu anachititsa kuti buku lililonse la m’Baibulo lipezeke m’chilankhulo chimene anthu ambiri ankagwiritsa ntchito, chomwe chinali chosavuta kumva. Potsatira zimenezi, Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano inatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso m’Chingelezi, mu October 2013. Mawu oyamba a Baibuloli amati: “Cholinga chathu chimakhala kutulutsa Baibulo logwirizana ndi zomwe zili m’mipukutu yoyambirira, lomveka bwino komanso losavuta kuwerenga.”

Baibulo la Dziko Latsopano la Chichewa linamasuliridwa kuchokera ku Baibulo lachingelezi la New World Translation of the Holy Scriptures​—lokonzedwanso mu 1984. Baibulo la Chichewa lokonzedwansoli, lomwe ndi losavuta kuwerenga, lamasuliridwa kuchokera ku Baibulo latsopano la Chingelezi ndipo likulowa m’malo mwa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika la Chichewa.

Komanso, kungoyambira pamene Baibulo la Chingelezi linatuluka, anthu akhala akumvetsa bwino kwambiri zilankhulo zoyambirira zimene Baibulo linalembedwa zomwe ndi Chiheberi, Chiaramu komanso Chigiriki. Panopa kwapezeka mipukutu yomwe kunalibe pa nthawi imene Baibulo la Dziko Latsopano linkatulutsidwa. Mipukutu imeneyi ikumathandiza omasulira Baibulo kudziwa mmene angamawerengere molondola mawu oyambirira a m’Baibulo.

Zotsatira zake n’zakuti mawu ena anasinthidwa kuti agwirizane ndi zimene akatswiri a Baibulo akuona kuti n’zolondola potengera mmene mawu oyambirira a m’Baibulo analembedwera. Mwachitsanzo, mogwirizana ndi mipukutu ina, lemba la Mateyu 7:13 limati: “Lowani pageti laling’ono. Chifukwa msewu umene ukupita kuchiwonongeko ndi wotakasuka komanso geti lake ndi lalikulu.” Mu Baibulo la Dziko Latsopano lakale munalibe mawu akuti, “geti lake.” Komabe, kufufuza mosamala mipukutu kunachititsa kuti zidziwike kuti m’Baibulo loyambirira mawu akuti, “geti lake” analimo. Choncho mawuwa anaikidwa m’Baibulo lokonzedwanso. Pali zinthu zambiri zimene zinasinthidwa pa chifukwa chofanana ndi chimenechi. Ngakhale zili choncho, kusintha kumeneku ndi kochepa ndipo sikukukhudzana ndi kusintha uthenga wa m’Mawu a Mulungu.

Kafukufuku wowonjezereka anasonyezanso kuti m’Baibulo muli malo enanso 6 omwe dzina la Mulungu liyenera kupezekamo. Malo amenewa ndi pa: Oweruza 19:18 ndi pa 1 Samueli 2:25; 6:3; 10:26; 23:14, 16. Tsopano m’Baibulo la Dziko Latsopano la Chingelezi mukupezeka dzina la Mulungu lakuti, Yehova, m’malo okwana 7,216 ndipo chiwerengerochi chikuphatikizapo malo 237 m’Malemba Achigiriki.

Ndi ndani amene akufalitsa Baibuloli?

Baibulo la Dziko Latsopano limafalitsidwa ndi bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society, lomwe ndi gulu lovomerezeka ndi malamulo loimira Mboni za Yehova. Kwa zaka zoposa 100, a Mboni za Yehova afalitsa Mabaibulo ambiri padziko lonse lapansi. Pakati pa zaka za 1950 ndi 1960, Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano inatulutsa Baibulo loyambirira la Chingelezi. Anthu amene anali m’Komiti imeneyi sanafune kuti atchuke, ndiye anapempha kuti mayina awo asadziwike ngakhale atamwalira.​—1 Akorinto 10:31.

Mu 2008, Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, linasankha gulu lina la abale kuti apange Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano. Nthawi yomweyo komitiyi inayamba ntchito yokonzanso Baibulo la Chingelezi poganizira zinthu zambiri zimene zasintha m’chilankhulo cha Chingelezi kungoyambira pamene Baibulo loyambirira linatuluka. Komitiyi inaganizira mosamala mayankho oposa 70,000 a mafunso omwe omasulira Baibulo la Dziko Latsopano m’zilankhulo zoposa 120 anafunsa.

Kodi ntchito yokonzanso Baibulo la Chichewa inachitika bwanji?

Choyamba, panasankhidwa gulu la Akhristu odzipereka kuti agwire ntchito yomasulirayi. Zaoneka kuti omasulira, amamasulira zinthu zomveka bwino kwambiri akamagwira ntchito yawo ali anthu angapo osati aliyense payekha. (Miyambo 11:14) Nthawi zambiri, aliyense mwa anthuwa amakhala kuti ali ndi luso kale lomasulira mabuku a Mboni za Yehova. Kenako omasulirawa analandira maphunziro okhudza mmene angagwirire ntchito yomasulira Baibulo komanso mmene angagwiritsire ntchito mapulogalamu apadera apakompyuta.

Omasulirawa anagwiritsa ntchito njira inayake yosavuta yomwe imaphatikiza mawu a m’Baibulo ndi pulogalamu yapakompyuta. Dipatimenti Yothandiza Omasulira yomwe ili ku New York, U.S.A., inkathandiza kwambiri omasulirawa. Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova limapitiriza kuyang’anira ntchito yomasulira Baibulo kudzera m’Komiti Yoona za Ntchito Yolemba Mabuku. Komano kodi ntchitoyi imagwiridwa bwanji?

Omasulirawa anapatsidwa malangizo akuti amasulire Baibulo (1) lolondola koma limene anthu wamba sangavutike kumva, (2) lotsatirika, komanso (3) amasulire liwu ndi liwu ngati zili zololeka m’chilankhulocho. Ndiye kodi anakwanitsa bwanji zimenezi? Tiyeni tione za Baibulo lomwe latulutsidwa kumeneli. Omasulirawa amayamba ndi kuona mawu omwe anagwiritsidwa ntchito m’Baibulo la Dziko Latsopano la Chichewa lomwe lilipo kale. Pulogalamu yapakompyuta yotchedwa Watchtower Translation System yomwe omasulira amagwiritsa ntchito imasonyeza mawu a m’Baibulo ofanana nawo omwe akugwirizana ndi nkhaniyo. Pulogalamuyi imasonyezanso mawu oyambirira a Chigiriki kapena Chiheberi kuti omasulira aone mmene mawuwa anamasuliridwira m’malo ena omwe akupezekamo. Zonsezi zinathandiza kuti apeze mawu a Chichewa ofanana nawo. Pogwiritsa ntchito njira imeneyi, omasulirawa anayesetsa kumasulira mogwirizana ndi mmene anthu amalankhulira komanso kupeza mawu a Chichewa ofanana nawo osavuta kumva pamene ankamasulira vesi lililonse.

N’zosachita kufunsa kuti ntchito yomasulira imafunika kuchita zinthu zambiri kuposa kungopeza mawu ofanana ndi omwe ali ku Chingelezi. Pamakhala ntchito yaikulu poonetsetsa kuti mawu a Chichewa omwe agwiritsidwa ntchito akhale oti akufotokoza molondola mfundo ya m’Malemba mogwirizana ndi nkhaniyo. Umboni wa zimenezi ndi Baibulo lomasuliridwa bwino lomwe latulutsidwali. Baibulo la Dziko Latsopano la Chichewa linamasulira Mawu a Mulungu molondola komanso ndi lomveka bwino ndiponso losavuta kuwerenga.

Tikukulimbikitsani kuti muwerenge Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika. Mungaliwerenge pa intaneti kapena pa JW Library, kapenanso mungakatenge Baibulo losindikizidwa kumpingo wa Mboni za Yehova wa komwe mumakhala. Muliwerenge ndi chikhulupiriro chonse kuti mawu a Mulungu amasuliridwa molondola m’chilankhulo chanu.

Zomwe zili mu Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso

Kodi M’Baibulo Muli Nkhani Zotani?: Mbali imeneyi ili ndi mavesi a m’Baibulo omwe akuyankha mafunso 20 okhudza ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo

Zimene Zili M’bukuli: Mbali imeneyi ikufotokoza mwachidule zokhudza buku la m’Baibulo lililonse kuti musamavutike kupeza nkhani za m’Baibulo. Mbali imeneyi ikulowa m’malo mwa timawu tam’mwamba tomwe tinkapezeka patsamba lililonse m’Baibulo lakale

Danga la Pakati: Pakumapezeka malifalensi okhawo omwe ndi othandiza kwambiri mu utumiki

Mawu Am’munsi: Pamapezeka njira zina zomasulira mawu, mawu omwe amasuliridwa liwu ndi liwu komanso mfundo zazikulu zofotokoza nkhani

Kalozera wa Mawu a M’Baibulo: Panopa muli mawu ndi mavesi amene amathandiza kwambiri polalikira ndi pophunzitsa

Matanthauzo a Mawu Ena a M’Baibulo: Mbali imeneyi ikufotokoza matanthauzo a mawu mahandiredi ambirimbiri omwe agwiritsidwa ntchito m’Baibulo

Zakumapeto A: Zikufotokoza mbali zina za m’Baibuloli monga kalembedwe kake, mawu amene asintha komanso malo amene dzina la Mulungu likupezeka

Zakumapeto B: Muli zigawo 15 zokhala ndi mapu komanso zithunzi zamitundu yosiyanasiyana

a Baibulo la Chichewa la Malemba Achigiriki linatulutsidwa mu 2006.