Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Gulu la Anthu Omasulira Mabuku a Mboni za Yehova M’Chisipanishi Lasamukira ku Spain

Gulu la Anthu Omasulira Mabuku a Mboni za Yehova M’Chisipanishi Lasamukira ku Spain

Yesu ananena kuti uthenga wabwino wa Ufumu udzalalikidwa kwa anthu padziko lonse lapansi. (Mateyu 24:14) Kuyambira mu 1909, mabuku othandiza anthu kumvetsa Baibulo ofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova anayamba kumasuliridwa m’Chisipanishi. Mabukuwa akhala akuthandiza anthu padziko lonse lapansi kumvetsa uthenga wa Ufumu m’chinenero chawo. Panopa Chisipanishi ndi chinenero chachiwiri chomwe anthu ambiri amalankhula monga chinenero chawo choyambirira, poyerekezera ndi Chitchainizi chomwe chimalankhulidwa ndi anthu ambiri zedi monga chinenero chawo choyambirira. Masiku ano, anthu pafupifupi hafu biliyoni amalankhula Chisipanishi.

Bambo William, omwe ali m’gulu la anthu omasulira Chisipanishi anati: “Chisipanishi ndi chinenero chomwe chimalankhulidwa m’mayiko ambiri ndi anthu azikhalidwe zosiyanasiyana. Cholinga chathu n’chakuti tizimasulira m’njira yoti munthu wina aliyense, kaya maphunziro ake ndi otani, kaya ndi wolemera kapena wosauka, azimva mosavuta mabuku athu.” Pofuna kuti zimenezi zitheke, anthu a m’gulu logwira ntchito yomasulira mabukuwa ndi ochokera m’mayiko osiyanasiyana monga Argentina, Colombia, El Salvador, Guatemala, Mexico, Puerto Rico, United States, Uruguay, Venezuela ndi Spain.

Kwa zaka zambiri, ntchito yomasulira mabuku a Mboni za Yehova m’Chisipanishi, yakhala ikuchitikira m’dziko la United States, mothandizidwa ndi omasulira a ku Argentina, Mexico, ndi Spain. Komabe mu 1993, gulu la anthu omasulira Chisipanishi, linasamukira ku Puerto Rico, n’cholinga choti onse azikagwira ntchito malo amodzi.

Mu March 2012, panakonzedwanso zoti gulu la anthu omasulira Chisipanishili lisamuke. Tsopano gululi linasamukira ku ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Spain. Bambo Edward anafotokoza kuti: “Sikuti panangofunika kusamutsa anthu ndi katundu ayi. Tinafunikanso kusamutsa chipangizo chofunika kwambiri pa ntchito yathu, chomwe ndi laibulale.” Laibulaleyi ili ndi mabuku pafupifupi 2,500, kuphatikizapo Mabaibulo mahandiredi ambiri a m’Chisipanishi.

Gulu la anthu omasulira Chisipanishi likulandiridwa ndi manja awiri ku Spain

Pa May 29, 2013, gulu la anthu omasulira mabuku m’Chisipanishi linafika ku ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Spain, ndipo linalandiridwa ndi manja awiri. Ntchito yosamutsa katundu ndiponso anthu, kudutsa panyanja ya mchere ya Atlantic, inagwiridwa mwadongosolo kwambiri. Ngakhale panali chintchito chachikulu chonchi, owerenga mabuku athu achisipanishi sanasokonezedwe mwanjira ina iliyonse. Bambo Edward anati: “Uthenga wa Ufumu ndi wofunika kwambiri, ndipo tikufuna kuti anthu ambiri olankhula Chisipanishi auwerenge.”