Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Dziko la Estonia Linayamikira Kwambiri Baibulo la Dziko Latsopano

Dziko la Estonia Linayamikira Kwambiri Baibulo la Dziko Latsopano

M’chaka cha 2014, dziko la Estonia linaika Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika m’gulu la zinthu zomwe zinalembedwa bwino kwambiri m’chaka chimenecho. Pagululi panali zinthu 18 ndipo Baibuloli linakhala pa nambala 3.

Baibulo latsopanoli linatulutsidwa pa 8 August, 2014, ndipo linasankhidwa kuti ndi Baibulo lolembedwa bwino kwambiri ndi katswiri wina wa chiyankhulo, dzina lake Kristiina Ross. Katswiriyu ananena kuti Baibulo la Dziko Latsopano ndi “lokoma powerenga komanso lomveka bwino.” Ananenanso kuti, “Anthu amene anamasulira Baibuloli ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa anthu amene amamasulira mabuku ku Estonia.” Pulofesa wina wa chiyankhulo komanso chikhalidwe cha anthu, dzina lake Rein Veidemann, ananena kuti anthu amene anamasulira Baibuloli anagwira “ntchito yotamandika kwambiri.”

Baibulo loyamba la Chiesitoniya linatulutsidwa mu 1739. Kungochokera nthawi imeneyo pakhala pakutulukanso Mabaibulo ena ambiri. Ndiye n’chifukwa chiyani anthu akuona kuti Baibulo la Dziko Latsopano ndi lamtengo wapatali komanso kuti anthu amene anagwira ntchito yolimasulira anagwira “ntchito yotamandika kwambiri”?

Ndi lolondola. M’Baibulo la Chiesitoniya lomwe linasindikizidwa mu 1988 muli dzina la Mulungu lakuti Yehova. Dzinali limapezeka ka 6,800 m’Malemba Achiheberi kapena kuti Chipangano Chakale. * Mu Baibulo la Dziko Latsopano mulinso dzinali ndipo limapezeka maulendo ochuluka kwambiri kuposa Baibulo limeneli. Koma chochititsa chidwi kwambiri n’choti mu Baibulo la Dziko Latsopano, dzinali limapezekanso m’Malemba Achigiriki Achikhristu kapena kuti Chipangano Chatsopano. Anthu amene anamasulira Baibuloli anachita zimenezi m’malo omwe zimachita kuonekeratu kuti dzinali linkapezeka m’mipukutu yakale.

Ndi lomveka bwino. Cholinga cha omasulira chimakhala kumasulira zinthu zolondola komanso zomveka bwino. Koma nthawi zambiri zimakhala zovuta kukwaniritsa zolinga ziwiri zonsezi. Ndiye kodi Baibulo la Dziko Latsopano la Chiesitoniya linakwaniritsa zolinga zonsezi? Katswiri wina womasulira Mabaibulo, dzina lake Toomas Paul, analemba m’nyuzipepala ina kuti Baibuloli “ndi lomveka bwino kwambiri ndipo lili ndi mawu amene anthu a ku Estonia amagwiritsa ntchito panopa.” Ananenanso kuti: “Ndikukuuzani kuti aka n’koyamba anthu kumasulira buku m’Chiesitoniya, n’kukhala lomveka bwino komanso lolondola chonchi.”

Dziko la Estonia linayamikira kwambiri Baibulo la Dziko Latsopano

Zikuonekanso kuti anthu ambiri a ku Estonia akusangalala ndi Baibuloli. Wailesi ya boma inaulutsa pulogalamu ya maminitsi 40 n’cholinga choti akambirane zokhudza Baibuloli. Atsogoleri a zipembedzo komanso anthu a m’zipembedzo zosiyanasiyana akumapempha a Mboni za Yehova kuti awagawire Baibuloli. Sukulu ina yotchuka ya mumzinda wa Tallinn inapempha Mabaibulo 20 a Baibulo la Dziko Latsopano kuti ophunzira azigwiritsa ntchito m’kalasi. Anthu a ku Estonia amakonda kuwerenga kwambiri, n’chifukwa chake a Mboni za Yehova anayesetsa kumasulira Baibulo lolondola komanso lomveka bwino kwambiri.

^ ndime 5 Tsiku lina munthu wina yemwe ndi tcheyamani woona za maphunziro a Chipangano Chatsopano pa yunivesite ya Tartu, dzina lake Ain Riistan, ankafotokoza mmene anthu anayambira kugwiritsa ntchito dzina lakuti Yehova ku Estonia. Atamaliza kunena zimenezi anati: “Ndikuona kuti dzina lakuti Yehova ndi loyenera kumaligwiritsa ntchito masiku ano. Ngakhale kuti katchulidwe kenikeni ka zilembo zomwe zimaimira dzinali sikadziwika bwinobwino, anthu anazolowera kutchula dzina lakuti Yehova, ndipo akhala akuchita zimenezi kuchokera kale kwambiri. Yehova ndi dzina la Mulungu amene anatumiza mwana wake kuti adzatiwombole.”